Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 15:28 - Buku Lopatulika

28 Ndipo Samuele ananena naye, Yehova anang'amba ufumu wa Israele lero kuuchotsa kwa inu, naupatsa kwa mnansi wanu wina wabwino woposa inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Ndipo Samuele ananena naye, Yehova anang'amba ufumu wa Israele lero kuuchotsa kwa inu, naupatsa kwa mnansi wanu wina wabwino woposa inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Apo Samuele adamuuza kuti, “Chauta wachita ngati kung'amba ufumu wa Israele kuchoka kwa inu lero, ndipo waupereka kwa mnzanu wabwino koposa inuyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Samueli anati kwa iye, “Yehova wangʼamba ufumu wanu kuchoka kwa inu, ndipo waupereka kwa mnzanu woposa inu.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 15:28
20 Mawu Ofanana  

kuchotsa ufumu kunyumba ya Saulo ndi kukhazika mpando wachifumu wa Davide pa Israele ndi pa Yuda, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.


chitani tsono, popeza Yehova analankhula za Davide, kuti, Ndi dzanja la Davide mnyamata wanga ndidzapulumutsa anthu anga Aisraele ku dzanja la Afilisti, ndi ku dzanja la adani ao onse.


Mulungu alange Abinere, naonjezepo, ndikapanda kumchitira Davide monga Yehova anamlumbirira;


Koma Davide ananena ndi Mikala, Ndatero pamaso pa Yehova, amene anandisankha ine ndi kupitirira atate wako ndi banja lake lonse, nandiika ndikhale mtsogoleri wa anthu a Yehova, wa Israele, chifukwa chake ndidzasewera pamaso pa Yehova.


Chifukwa chake Yehova ananena ndi Solomoni, Popeza chinthu ichi chachitika ndi iwe, ndipo sunasunge chipangano changa ndi malemba anga amene ndinakulamulira, zedi, ndidzakung'ambira ufumu ndi kuupatsa mnyamata wako.


osafunsira kwa Yehova; chifukwa chake anamupha, napambutsira ufumu kwa Davide mwana wa Yese.


Aphwanya eni mphamvu osatulutsa kubwalo mlandu wao, naika ena m'malo mwao.


Chitsutso ichi adachilamulira amithenga oyerawo, anachifunsa, nachinena, kuti amoyo adziwe kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna, nauutsira wolubukira anthu.


Nadzakuinga kukuchotsa kwa anthu, ndi pokhala pako udzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo; adzakudyetsa udzu ngati ng'ombe; ndipo zidzakupitira nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka udzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.


Yesu anamyankha iye, Simukadakhala nao ulamuliro uliwonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kuchokera Kumwamba; chifukwa cha ichi iye wondipereka Ine kwa inu ali nalo tchimo loposa.


Ndipo m'mene atamchotsa iye, anawautsira Davide akhale mfumu yao; amenenso anamchitira umboni, nati, Ndapeza Davide, mwana wa Yese, munthu wa pamtima panga, amene adzachita chifuniro changa chonse.


Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu.


Koma tsopano ufumu wanu sudzakhala chikhalire; Yehova wadzifunira munthu wa pamtima pake; ndipo Yehova wamuika iye akhale mtsogoleri wa anthu ake, chifukwa inu simunasunge chimene Yehova anakulamulirani.


Ndipo anatumiza munthu, nabwera naye. Tsono iye anali wofiirira, ndi wa nkhope yokongola, ndi maonekedwe okoma. Ndipo Yehova anati, Nyamuka umdzoze, pakuti ndi ameneyu.


Koma Saulo anakwiya ndithu, ndi kunenaku kunamuipira; nati, Kwa Davide anawerengera zikwi zankhani, koma kwa ine zikwi zokha; chimperewera nchiyaninso, koma ufumu wokha?


Ndipo kudzali, pamene Yehova anachitira mbuye wanga monga mwa zabwino zonse adalankhula za inu, ndipo adadzaika inu mukhale kalonga wa Israele;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa