Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 9:16 - Buku Lopatulika

16 Mawa, monga dzuwa lino, ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini, udzamdzoza iye akhale mtsogoleri wa anthu anga Israele, kuti akawapulumutse anthu anga m'manja a Afilisti; pakuti Ine ndinapenya pa anthu anga, popeza kulira kwao kunandifika Ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Mawa, monga dzuwa lino, ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini, udzamdzoza iye akhale mtsogoleri wa anthu anga Israele, kuti akawapulumutse anthu anga m'manja a Afilisti; pakuti Ine ndinapenya pa anthu anga, popeza kulira kwao kunandifika Ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 “Maŵa nthaŵi yonga yomwe ino, ndidzakutumizira munthu wa ku dera la Benjamini, udzamudzoze kuti akhale mfumu ya anthu anga Aisraele. Adzapulumutsa anthu kwa Afilisti. Ndaona kuzunzika kwao, ndipo ndamva kulira kwao.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 “Mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini. Udzamudzoze kuti akhale mtsogoleri wa anthu anga, Aisraeli. Iye adzawapulumutsa mʼdzanja la Afilisti. Ine ndaona kuzunzika kwawo ndipo ndamva kulira kwawo.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 9:16
17 Mawu Ofanana  

chitani tsono, popeza Yehova analankhula za Davide, kuti, Ndi dzanja la Davide mnyamata wanga ndidzapulumutsa anthu anga Aisraele ku dzanja la Afilisti, ndi ku dzanja la adani ao onse.


Bwerera, nunene kwa Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga, Atero Yehova Mulungu wa Davide kholo lako, Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, ndidzakuchiritsa, tsiku lachitatu udzakwera kunka kunyumba ya Yehova.


Yehova, imvani pemphero langa, ndipo mfuu wanga ufikire Inu.


Koma anapenya nsautso yao, pakumva kufuula kwao:


Penyani mazunzo anga ndi zovuta zanga; ndipo khululukirani zolakwa zanga zonse.


Mtima wa munthu ulingalira njira yake; koma Yehova ayendetsa mapazi ake.


Ndipo Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga anadza kwa ine m'bwalo la kaidi monga mwa mau a Yehova, nati kwa ine, Gulatu munda wanga, wa ku Anatoti, m'dziko la Benjamini; pakuti mphamvu yakulowa ndi yakuombola ndi yako; udzigulire wekha. Pamenepo ndinadziwa kuti awa ndi mau a Yehova.


Pamenepo Samuele anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pake, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozeni ndi Yehova kodi, Mukhale mfumu ya pa cholowa chake?


Ndipo Saulo ndi anthu onse amene anali naye anaunjikana pamodzi, natulukira kunkhondoko; ndipo taonani, munthu yense anakantha mnzake ndi lupanga, ndipo panali kusokonezeka kwakukulu.


Chomwecho Yehova anapulumutsa Israele tsiku lija; ndipo nkhondo inapitirira pa Betaveni.


Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Yehova ananditumiza ine kukudzozani mukhale mfumu ya anthu ake Aisraele; chifukwa chake tsono mumvere kunena kwa mau a Yehova.


Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Iwe ukuti ulire chifukwa cha Saulo nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israele? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Yese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ake.


Ndipo uitane Yese abwere kunsembeko, ndipo Ine ndidzakusonyeza chimene uyenera kuchita; ndipo udzandidzozera iye amene ndidzakutchulira dzina lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa