Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 13:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Munachita kopusa; simunasunge lamulo la Yehova Mulungu wanu, limene Iye anakulamulirani; mwenzi Yehova atakhazikitsa nthawi ino ufumu wanu, ukhale pa Israele nthawi yosatha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Munachita kopusa; simunasunga lamulo la Yehova Mulungu wanu, limene Iye anakulamulirani; mwenzi Yehova atakhazikitsa nthawi yino ufumu wanu, ukhale pa Israele nthawi yosatha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Apo Samuele adamuuza kuti, “Mwachitatu zopusa. Simudatsate zimene Chauta, Mulungu wanu, adakulamulani. Mukadazitsata, bwenzi Chauta atakhazikitsa ufumu wanu pakati pa Aisraele mpaka muyaya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Samueli anati, “Mwachita zopusa. Simunatsate zimene Yehova Mulungu wanu anakulamulani kuti muchite. Mukanazitsata, Yehova akanawukhazikitsa ufumu wanu mu Israeli mpaka kalekale.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 13:13
23 Mawu Ofanana  

Ndipo sunandiloleze ine ndimpsompsone ana anga aamuna ndi aakazi? Wapusa iwe pakuchita chotero.


Pamenepo mtima wa Davide unamtsutsa, atatha kuwerenga anthuwo. Davide nati kwa Yehova, Ndinachimwa kwakukulu ndi chinthu chimene ndinachita; koma tsopano Yehova muchotse mphulupulu ya mnyamata wanu, pakuti ndinachita kopusa ndithu.


Nati iye, Sindimavute Israele ine ai, koma inu ndi nyumba ya atate wanu; popeza munasiya malamulo a Yehova, ndi kutsata Abaala.


Ndipo Ahabu anati kwa Eliya, Wandipeza kodi, mdani wangawe? Nayankha, Ndakupeza; pokhala wadzigulitsa kuchita choipacho pamaso pa Yehova.


Momwemo Saulo anafa, chifukwa cha kulakwa kwake analakwira Yehova, kulakwira mau a Yehova amene sanawasunge; ndiponso chifukwa cha kufunsira wobwebweta, kufunsirako,


Pakuti maso a Yehova ayang'ana uko ndi uko m'dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi Iye. Mwachita chopusa m'menemo; pakuti kuyambira tsopano mudzaona nkhondo.


Natuluka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza zoipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova.


Kodi kuyenera kunena kwa mfumu, Wopanda pake iwe, kapena kwa akalonga, Oipa inu?


Munthu amatamandidwa monga mwa nzeru yake; koma wokhota mtima adzanyozedwa.


Utsiru wa munthu ukhotetsa njira yake; mtima wake udandaula pa Yehova.


Ndipo Yesaya anati kwa Hezekiya, Imvani mau a Yehova wa makamu.


koma ukachita choipa pamaso panga, osamvera mau anga, pamenepo ndidzaleka chabwinocho, ndidati ndiwachitire.


Koma Hana sadakwere, chifukwa kuti anati kwa mwamuna wake Sindidzakwerako kufikira mwanayo ataleka kuyamwa, pamenepo ndidzapita naye kuti aoneke pamaso pa Yehova, ndi kukhalako chikhalire.


chifukwa chake ndinati, Afilisti adzatitsikira pano pa Giligala, ndisanapembedze Yehova; potero ndinadzifulumiza, ndi kupereka nsembe yopsereza.


Kundichititsa chisoni kuti ndinaika Saulo akhale mfumu; pakuti wabwerera wosanditsata Ine, ndipo sanachite malamulo anga. Ndipo Samuele anakwiya; nalira kwa Yehova usiku wonse.


Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.


Ndipo Samuele ananena naye, Yehova anang'amba ufumu wa Israele lero kuuchotsa kwa inu, naupatsa kwa mnansi wanu wina wabwino woposa inu.


Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Iwe ukuti ulire chifukwa cha Saulo nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israele? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Yese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ake.


Pamenepo Saulo anati, Ndinachimwa; bwera, mwana wanga Davide; pakuti sindidzakuchitiranso choipa, popeza moyo wanga unali wa mtengo wapatali pamaso pako lero; ona, ndinapusa ndi kulakwa kwakukulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa