Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 12:22 - Buku Lopatulika

Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake chifukwa cha dzina lake lalikulu; pakuti kudamkomera Yehova kukuyesani inu anthu a Iye yekha.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake chifukwa cha dzina lake lalikulu; pakuti kudamkomera Yehova kukuyesani inu anthu a Iye yekha.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chauta sadzataya anthu ake, kuti dzina lake lalikulu linganyozeke, poti chidamukondweretsa kuti akusandutseni anthu ake.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yehova adzakana anthu ake kuopa kuti dzina lake lamphamvu linganyozeke, pakuti chinamukondweretsa Yehova kuti akusandutseni inu kukhala anthu ake.

Onani mutuwo



1 Samueli 12:22
49 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzakhala pakati pa ana a Israele osawasiya anthu anga a Israele.


Yehova Mulungu wathu akhale nafe monga umo anakhalira nao makolo athu, asatisiye kapena kutitaya;


Ndipo Yehova sadanene kuti adzafafaniza dzina la Israele pansi pa thambo; koma anawapulumutsa ndi dzanja la Yerobowamu mwana wa Yehowasi.


Ndipo ndidzataya chotsala cha cholowa changa, ndi kuwapereka m'dzanja la adani ao, nadzakhala iwo chakudya ndi chofunkha cha adani ao onse;


Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha.


ndipo anatuluka kukomana naye Asa, nanena naye, Mundimvere, Asa, ndi onse Ayuda ndi Abenjamini, Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye, mukamfuna Iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani.


nakana kumvera, osakumbukiranso zodabwitsa zanu munazichita pakati pao; koma anaumitsa khosi lao, ndipo m'kupanduka kwao anaika mtsogoleri abwerere kunka ku ukapolo wao; koma Inu ndinu Mulungu wokhululukira, wachisomo, ndi wansoni, wolekereza, ndi wochuluka chifundo; ndipo simunawasiye.


Koma anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake, kuti adziwitse chimphamvu chake.


Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake, ndipo sadzataya cholowa chake.


Akaneneranji Aejipito, ndi kuti, Anawatulutsa ndi cholinga choipa, kuti awaphe m'mapiri, ndi kuwatha pankhope padziko lapansi? Pepani, lekani choipacho cha pa anthu anu.


Pakuti ndidzatchinjiriza mzinda uno, kuupulumutsa, chifukwa cha Ine mwini, ndi mtumiki wanga Davide.


Wosauka ndi wosowa afuna madzi, ndipo palibe, ndi lilime lao lilephera, chifukwa cha ludzu; Ine Yehova ndidzawayankha, Ine Mulungu wa Israele sindidzawasiya.


Ndipo ndidzayendetsa akhungu m'khwalala, limene iwo salidziwa, m'njira zimene iwo sazidziwa ndidzawatsogolera; ndidzawalitsa mdima m'tsogolo mwao, ndi kulungamitsa malo okhota. Zinthu izi Ine ndidzachita, ndipo sindidzawasiya.


Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira machimo ako.


yense wotchedwa dzina langa, amene ndinamlenga chifukwa cha ulemerero wanga; ndinamuumba iye; inde, ndinampanga iye.


Chifukwa cha Ine ndekha, chifukwa cha Ine ndekha ndidzachita ichi, pakuti dzina langa lidetsedwerenji? Ndi ulemerero wanga sindidzaupereka kwa wina.


Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana wombala iye? Inde awa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe.


Pakuti anati, Zoonadi iwo ndiwo anthu anga, ana amene sangachite monyenga; chomwecho Iye anali Mpulumutsi wao.


Musatinyoze ife, chifukwa cha dzina lanu; musanyazitse mpando wachifumu wa ulemerero wanu; mukumbukire musasiye pangano lanu lopangana ndi ife.


Zingakhale zoipa zathu zititsutsa ife, chitani Inu chifukwa cha dzina lanu, Yehova; pakuti zobwerera zathu zachuluka; takuchimwirani Inu.


Bwanji mukhala ngati munthu wodabwa, ngati munthu wamphamvu wosatha kupulumutsa? Koma Inu, Yehova, muli pakati pathu, titchedwa ndi dzina lanu; musatisiye.


Bwanji mutiiwala chiiwalire, ndi kutisiya masiku ambirimbiri.


Koma ndinachichita chifukwa cha dzina langa, kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu amene ndinawatulutsa pamaso pao.


Koma ndinachichita chifukwa cha dzina langa, kuti lisadetsedwe pamaso pa amitundu amene anakhala pakati pao, amene pamaso pao ndinadzidziwitsa kwa iwo, pakuwatulutsa m'dziko la Ejipito.


Ndakukondani, ati Yehova; koma inu mukuti, Mwatikonda motani? Esau si mkulu wake wa Yakobo kodi? Ati Yehova; ndipo ndinakonda Yakobo;


eetu, Atate, chifukwa chotero chinakhala chokondweretsa pamaso panu.


Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.


Chifukwa chake ndinena, Mulungu anataya anthu ake kodi? Msatero ai. Pakuti inenso ndili Mwisraele, wa mbeu ya Abrahamu, wa fuko la Benjamini.


Pakuti mphatso zake ndi kuitana kwake kwa Mulungu sizilapika.


Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandire?


kuti ife amene tinakhulupirira Khristu kale tikayamikitse ulemerero wake.


kuti uyamikidwe ulemerero wa chisomo chake, chimene anatichitira ife kwaufulu mwa Wokondedwayo.


Popeza ndinu mtundu wa anthu opatulikira Yehova Mulungu wanu, ndipo Yehova anakusankhani mukhale mtundu wa anthu wa pa wokha wa Iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu okhala pankhope padziko lapansi.


Pamenepo ndidzawapsera mtima tsiku ilo, ndipo ndidzawataya, ndi kuwabisira nkhope yanga, ndipo adzathedwa, ndi zoipa ndi zovuta zambiri zidzawafikira; kotero kuti adzati tsiku lija, Sizitifikira kodi zoipa izi popeza Mulungu wathu sakhala pakati pa ife?


Khalani amphamvu, limbikani mitima, musamachita mantha, kapena kuopsedwa chifukwa cha iwowa; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; Iye sadzakusowani, kapena kukusiyani.


Ndipo Yehova, Iye ndiye amene akutsogolera; Iye adzakhala ndi iwe, Iye sadzakusowa kapena kukusiya; usamachita mantha, usamatenga nkhawa.


Pakuti inu ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu; Yehova Mulungu wanu anakusankhani, mukhale mtundu wa pa wokha wa Iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu akukhala pa nkhope ya dziko.


Simulowa kulandira dziko lao chifukwa cha chilungamo chanu, kapena mtima wanu woongoka; koma Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu chifukwa cha zoipa za amitundu awa, ndi kuti akhazikitse mau amene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo.


pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;


Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.


Akadzamva ichi Akanani ndi okhala m'dziko onse, adzatizinga ndi kuduliratu dzina lathu padziko lapansi; ndipo mudzachitiranji dzina lanu lalikulu?


Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;