Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 94:14 - Buku Lopatulika

14 Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake, ndipo sadzataya cholowa chake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake, ndipo sadzataya cholandira chake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Chauta sadzaŵataya anthu ake, sadzaŵasiya okha osankhidwa ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Pakuti Yehova sadzawakana anthu ake; Iye sadzasiya cholowa chake.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 94:14
19 Mawu Ofanana  

Munthu wokhumba moyo ndani, wokonda masiku, kuti aone zabwino?


Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.


Kumbukirani msonkhano wanu, umene munaugula kale, umene munauombola ukhale fuko la cholowa chanu; Phiri la Ziyoni limene mukhalamo.


Aphwanya anthu anu, Yehova, nazunza cholowa chanu.


Wosauka ndi wosowa afuna madzi, ndipo palibe, ndi lilime lao lilephera, chifukwa cha ludzu; Ine Yehova ndidzawayankha, Ine Mulungu wa Israele sindidzawasiya.


Gawo la Yakobo silifanana ndi iwo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndiye mtundu wa cholowa chake; dzina lake ndi Yehova wa makamu.


Ndiponso pali ichinso: pokhala iwo m'dziko la adani ao sindidzawakaniza, kapena kunyansidwa nao, kuwaononga konse, ndi kuthyola pangano langa ndinapangana nao; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wao.


ndipo amene Iye anawalamuliratu, iwo anawaitananso; ndimo iwo amene Iye anawaitana, iwowa anawayesanso olungama; ndi iwo amene Iye anawayesa olungama, iwowa anawapatsanso ulemerero.


ndiko kunena kuti maso a mitima yanu awalitsike, kuti mukadziwe inu chiyembekezo cha kuitana kwake nchiyani; chiyaninso chuma cha ulemerero wa cholowa chake mwa oyera mtima,


Khalani amphamvu, limbikani mitima, musamachita mantha, kapena kuopsedwa chifukwa cha iwowa; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; Iye sadzakusowani, kapena kukusiyani.


Ndipo Yehova, Iye ndiye amene akutsogolera; Iye adzakhala ndi iwe, Iye sadzakusowa kapena kukusiya; usamachita mantha, usamatenga nkhawa.


Pakuti gawo la Yehova ndilo anthu ake; Yakobo ndiye muyeso wa cholowa chake.


Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.


Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake chifukwa cha dzina lake lalikulu; pakuti kudamkomera Yehova kukuyesani inu anthu a Iye yekha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa