Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa

Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano


Masalimo 60 - Buku Lopatulika Buku Lopatulika
Masalimo 60

Madandaulo ndi pempho la Davide
Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Susan-Eduti. Mikitamu wa Davide; lakulangiza; muja analimbana nao Aramu Naharaimu ndi Aramu Zoba, nabwera Yowabu anapha a Edomu kuchigwa cha Mchere zikwi khumi mphambu ziwiri.

1 Mwatitaya Mulungu, mwatipasula; mwakwiya; tibwezereni.

2 Mwagwedeza dziko, mwaling'amba. Konzani ming'alu yake; pakuti ligwedezeka.

3 Mwaonetsa anthu anu zowawa, mwatimwetsa vinyo wotinjenjemeretsa.

4 Koma mwapatsa mbendera akuopa Inu, aikweze chifukwa cha choonadi.

5 Kuti okondedwa anu alanditsidwe, pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja, ndipo mutivomereze.

6 Mulungu walankhula m'chiyero chake; ndidzakondwerera, ndidzagawa Sekemu, ndidzayesa muyeso chigwa cha Sukoti.

7 Giliyadi ndi wanga, Manasenso ndi wanga; ndipo Efuremu ndi mphamvu ya mutu wanga; Yuda ndiye wolamulira wanga.

8 Mowabu ndiye mkhate wanga; pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga. Filistiya, fuulatu chifukwa cha ine.

9 Adzandifikitsa ndani m'mzinda wa m'linga? Adzanditsogolera ndani ku Edomu?

10 Si ndinu, Mulungu, amene mwatitaya? Osatuluka nao makamu athu, Mulungu.

11 Tithandizeni kunsautso; kuti chipulumutso cha munthu ndi chabe.

12 Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima, ndipo Iye adzapondereza otisautsa.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi