Davide aneneratu za chionongeko cha oipa, iye nakhulupirira MulunguKwa Mkulu wa Nyimbo. Chilangizo cha Davide; muja analowa Doegi Mwedomu nauza Saulo nati kwa iye, Davide walowa m'nyumba ya Ahimeleki. 1 Udzitamandiranji ndi choipa, chiphona iwe? Chifundo cha Mulungu chikhala tsiku lonse. 2 Lilime lako likupanga zoipa; likunga lumo lakuthwa, lakuchita monyenga. 3 Ukonda choipa koposa chokoma; ndi bodza koposa kunena chilungamo, 4 ukonda mau onse akuononga, lilime lachinyengo, iwe. 5 Potero Mulungu adzakupasula kunthawi zonse, adzakuchotsa nadzakukwatula m'hema mwako, nadzakuzula, kukuchotsa m'dziko la amoyo. 6 Ndipo olungama adzachiona, nadzaopa, nadzamseka, ndi kuti, 7 Tapenyani, suyu munthuyu amene sanamuyese Mulungu mphamvu yake; amene anatama kuchuluka kwa chuma chake, nadzilimbitsa m'kuipsa kwake. 8 Koma ine ndine ngati mtengo wauwisi wa azitona m'nyumba ya Mulungu. Ndikhulupirira chifundo cha Mulungu kunthawi za nthawi. 9 Ndidzakuyamikani kosatha, popeza Inu munachichita ichi, ndipo ndidzayembekeza dzina lanu, pakuti ichi nchokoma, pamaso pa okondedwa anu. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi