Kusayamika kwa Israele; machenjezo ndi malonjezo1 Pamene Israele anali mwana, ndinamkonda, ndinaitana mwana wanga ali mu Ejipito. 2 Monga anawaitana, momwemo anawachokera; anaphera nsembe Abaala, nafukizira mafano osema. 3 Koma Ine ndinaphunzitsa Efuremu kuyenda, ndinawafungata m'manja mwanga; koma sanadziwe kuti ndinawachiritsa. 4 Ndinawakoka ndi zingwe za munthu, ndi zomangira za chikondi; ndinakhala nao ngati iwo akukweza goli pampuno pao, ndipo ndinawaikira chakudya. 5 Iye sadzabwerera kunka kudziko la Ejipito, koma Asiriya adzakhala mfumu yake, popeza anakana kubwera. 6 Ndi lupanga lidzagwera mizinda yake, lidzatha mipiringidzo yake, ndi kuononga chifukwa cha uphungu wao. 7 Ndipo anthu anga alimbika kubwerera m'mbuyo kundileka Ine; chinkana akawaitana atsate Iye ali m'mwamba, sadzakweza ndi mmodzi yense. 8 Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele? Ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? Ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? Mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi. 9 Sindidzachita mkwiyo wanga waukali, sindidzabwerera kuononga Efuremu; pakuti Ine ndine Mulungu, si munthu ai; Woyera wa pakati pako; ndipo sindidzalowa m'mzinda. 10 Adzatsata Yehova, Iye adzabangula ngati mkango; pamene abangula, ana adzafika ndi kunjenjemera kuchokera kumadzulo. 11 Adzafika ndi kunjenjemera ngati mbalame ya ku Ejipito, ndi ngati nkhunda m'dziko la Asiriya; ndipo ndidzawakhalitsa m'nyumba zao, ati Yehova 12 Efuremu andizinga ndi bodza, ndi nyumba ya Israele ndi chinyengo, ndi Yuda apikisana ndi Mulungu, ndiye Woyera wokhulupirika. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi