Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 11:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo anthu anga alimbika kubwerera m'mbuyo kundileka Ine; chinkana akawaitana atsate Iye ali m'mwamba, sadzakweza ndi mmodzi yense.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo anthu anga alimbika kubwerera m'mbuyo kundileka Ine; chinkana akawaitana atsate Iye ali m'mwamba, sadzakweza ndi mmodzi yense.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Anthu anga akangamira zondipandukira Ine. Tsono adzalira chifukwa cha goli lachilango limene lili pa iwo, koma palibe amene adzaŵachotsere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Anthu anga atsimikiza zondifulatira Ine. Ngakhale atayitana Wammwambamwamba, sizidzatheka kuti Iye awakwezenso.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 11:7
18 Mawu Ofanana  

Koma anthu anga sanamvere mau anga; ndipo Israele sanandivomere.


Wobwerera m'mbuyo m'mtima adzakhuta njira yake; koma munthu wabwino adzakhuta za mwa iye yekha.


Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira chilungamo; m'dziko la machitidwe oongoka, iye adzangochimwa, sadzaona chifumu cha Yehova.


Zingakhale zoipa zathu zititsutsa ife, chitani Inu chifukwa cha dzina lanu, Yehova; pakuti zobwerera zathu zachuluka; takuchimwirani Inu.


Choipa chako chidzakulanga iwe, mabwerero ako adzakudzudzula iwe; dziwa, nuone, kuti ichi ndi choipa ndi chowawa, kuti wasiya Yehova Mulungu wako, ndi kuti kundiopa Ine sikuli mwa iwe, ati Ambuye, Yehova wa makamu.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Israele wobwerera anadzionetsa wolungama kopambana ndi Yuda wonyenga.


Chiyambire tsiku limene makolo anu anatuluka m'dziko la Ejipito kufikira lero lino, ndatumiza kwa inu atumiki anga onse, aneneri, tsiku ndi tsiku, kuuka mamawa ndi kuwatumiza iwo;


koma sanandimvere Ine sanatchere khutu lao, koma anaumitsa khosi lao; anaipa koposa makolo ao.


Bwanji abwerera anthu awa a Yerusalemu chibwererere? Agwiritsa chinyengo, akana kubwera.


Monga anawaitana, momwemo anawachokera; anaphera nsembe Abaala, nafukizira mafano osema.


Ndidzachiritsa kubwerera kwao, ndidzawakonda mwaufulu; pakuti mkwiyo wanga wamchokera.


Pakuti Israele wachita kuuma khosi ngati ng'ombe yaikazi yaing'ono youma khosi; tsopano Yehova adzawadyetsa ngati mwanawankhosa kuthengo lalikulu.


Abwerera, koma si kwa Wam'mwambayo; akunga uta wosakhulupirika; akalonga ao adzagwa ndi lupanga mwa chipongwe cha lilime lao; ichi ndicho adzawasekera m'dziko la Ejipito.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa