Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 11:8 - Buku Lopatulika

8 Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele? Ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? Ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? Mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele? Ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? Ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? Mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 “Kodi ndingakusiye bwanji iwe Efuremu? Kodi ndingathe kukutaya bwanji iwe Israele? Kodi ndingathe bwanji kukusandutsa ngati Adima? Kodi ndingathe kukuwononga ngati Zeboimu? Mtima wanga wakana kutero, chifundo changa chikukula.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 “Kodi ndingakusiye bwanji iwe Efereimu? Kodi ndingakupereke bwanji iwe Israeli? Kodi ndingakuchitire bwanji zimene ndinachitira Adima? Kodi ndingathe bwanji kukuchitira zimene ndinachitira Zeboimu? Mtima wanga wakana kutero; chifundo changa chonse chikusefukira.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 11:8
38 Mawu Ofanana  

Ndipo anatuluka mfumu ya Sodomu, ndi ya Gomora, ndi mfumu ya Adima, ndi mfumu ya Zeboimu, ndi mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zowari) ndipo anawathira nkhondo m'chigwa cha Sidimu;


Ndipo pamene mthenga anatambasulira dzanja lake ku Yerusalemu kuuononga, choipacho chinachititsa Yehova chisoni, Iye nauza mthenga wakuononga anthuwo, kuti, Kwafikira tsopano, bweza dzanja lako. Ndipo mthenga wa Yehova anali pa dwale la Arauna Myebusi.


Koma mkazi amene mwana wamoyo anali wake analankhula ndi mfumu, popeza mtima wake unalira mwana wake, nati, Ha? Mbuye wanga, mumpatse uyo mwana wamoyo osamupha konse. Koma winayo anati, Asakhale wanga kapena wako, dulani.


Koma Yehova analeza nao mtima, nawachitira chifundo, nawatembenukira; chifukwa cha chipangano chake ndi Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, wosafuna kuwaononga, kapena kuwatayiratu pankhope pake.


Ndipo Yehova Mulungu wa makolo ao anatumiza kwa iwo ndi dzanja la mithenga yake, nalawirira mamawa kuituma, chifukwa anamvera chifundo anthu ake, ndi pokhala pake;


Ndipo anawakumbukira chipangano chake, naleza monga mwa kuchuluka kwa chifundo chake.


Chifukwa chake m'mimba mwanga mulirira Mowabu, ngati mngoli, ndi za m'mtima mwanga zilirira Kiriheresi.


Tayang'anani kunsi kuchokera kumwamba, taonani pokhala panu poyera, ndi pa ulemerero wanu, changu chanu ndi ntchito zanu zamphamvu zili kuti? Mwanditsekerezera zofunafuna za mtima wanu ndi chisoni chanu.


ngati mtundu umene, ndaunenera, udzatembenuka kuleka choipa chao, ndidzaleka choipacho ndidati ndiwachitire.


Pita; nulalikire mau awa kuyang'ana kumpoto, ndi kuti, Bwera iwe Israele wobwerera, ati Yehova; sindidzakuyang'anira iwe ndi kukwiya; pakuti Ine ndili wachifundo, ati Yehova, sindidzakhala nako kukwiya kunthawi zonse.


Kodi Efuremu ndiye mwana wanga wokondedwa? Kodi ndiye mwana wokondweretsa? Nthawi zonse zoti ndimnenera zomtsutsa, pakuti ndimkumbukiranso ndithu; chifukwa chake mumtima mwanga ndimlirira; ndidzamchitiradi chifundo, ati Yehova.


Ngati mudzakhalabe m'dziko muno, ndidzamangitsa mudzi wanu, osakugumulani, ndidzakuokani inu, osakuzulani; pakuti ndagwidwa nacho chisoni choipa chimene ndakuchitirani inu.


Ukhala pakati pa manyengo m'manyengo; akana kundidziwa, ati Yehova.


Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzawasungunula, ndi kuwayesa, pakuti ndidzachitanji, chifukwa cha mwana wamkazi wa anthu anga?


Onani, Yehova; pakuti ndavutika, m'kati mwanga mugwedezeka; mtima wanga wasanduka mwa ine; pakuti ndapikisana nanu ndithu; kunjako lupanga limangopha ana; m'nyumba muli imfa.


Angakhale aliritsa, koma adzachitira chisoni monga mwa kuchuluka kwa zifundo zake.


Pakuti samasautsa dala, ngakhale kumvetsa ana a anthu chisoni.


Uziti nao, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israele?


Pamenepo akupulumuka anu adzandikumbukira Ine kwa amitundu kumene anatengedwa ndende, kuti ndasweka ndi mtima wao wachigololo wolekana ndi Ine, ndi maso ao achigololo akutsata mafano ao; ndipo iwo adzakhala onyansa pamaso pao pa iwo eni, chifukwa cha zoipa anazichita m'zonyansa zao zonse.


Efuremu iwe, ndidzakuchitira chiyani? Yuda iwe, ndikuchitire chiyani? Pakuti kukoma mtima kwako kukunga mtambo wam'mawa ndi ngati mame akuphawa mamawa.


M'mene ndichiritsa Israele, mphulupulu ya Efuremu ivumbuluka, ndi zoipa za Samariya; pakuti achita bodza, ndipo mkhungu alowa m'nyumba, ndi gulu la mbala lilanda kubwalo.


Ndinagubuduza ena mwa inu, monga umo Mulungu anagubuduzira Sodomu ndi Gomora; ndipo inu munali ngati muuni wofumulidwa kumoto; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


Ndipo Yehova anachileka. Sichidzachitika, ati Yehova.


Ndipo Yehova anachileka. Ichi chomwe sichidzachitika, ati Ambuye Yehova.


Chifukwa chake Iye adzawapereka kufikira nthawi yoti wobalayo wabala; pamenepo otsala a abale ake adzabwera pamodzi ndi ana a Israele.


Chifukwa chake, pali moyo wanga, ati Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Zedi Mowabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pochuluka khwisa ndi maenje a mchere, ndi bwinja losatha; otsala a anthu anga adzalanda zao, ndi otsala a mtundu wa anthu anga adzawalandira akhale cholowa chao.


Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m'mapiko ake, koma inu simunafune ai!


Ndipo mbadwo ukudza, ana anu akuuka mutafa inu, ndi mlendo wochokera ku dziko lakutali, adzati, pakuona iwo miliri ya dziko ili, ndi nthendazi, Yehova awadwalitsa nazo.


Ndi kuti lidapsa dziko lake lonse ndi sulufure, ndi mchere, kuti sabzalamo, kapena siliphukitsa kanthu kapena sumerapo msipu, monga kupasula kwake kwa Sodomu ndi Gomora, Adima, ndi Zeboimu, imene Yehova anaipasula m'mkwiyo wake ndi ukali wake;


Popeza Yehova adzaweruza anthu ake, nadzachitira nsoni anthu ake; pakuona Iye kuti mphamvu yao yatha, wosatsala womangika kapena waufulu.


ndipo pakuisandutsa makala mizinda ya Sodomu ndi Gomora anaitsutsa poigwetsa, ataiika chitsanzo cha kwa iwo akakhala osapembedza;


Monga Sodomu ndi Gomora, ndi mizinda yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kutsata zilakolako zachilendo, iikidwa chitsanzo, pakuchitidwa chilango cha moto wosatha.


Ndipo mitembo yao idzakhala pa khwalala lamzinda waukulu, umene utchedwa, ponena zachizimu, Sodomu ndi Ejipito, pameneponso Ambuye wao anapachikidwa.


nafuula poona utsi wa kutentha kwake, nanena, Mzinda uti ufanana ndi mzinda waukuluwo?


Pamenepo anachotsa milungu yachilendo pakati pao, natumikira Yehova; ndipo mtima wake unagwidwa chisoni chifukwa cha mavuto a Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa