Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 11:11 - Buku Lopatulika

11 Adzafika ndi kunjenjemera ngati mbalame ya ku Ejipito, ndi ngati nkhunda m'dziko la Asiriya; ndipo ndidzawakhalitsa m'nyumba zao, ati Yehova

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Adzafika ndi kunjenjemera ngati mbalame ya ku Ejipito, ndi ngati nkhunda m'dziko la Asiriya; ndipo ndidzawakhalitsa m'nyumba zao, ati Yehova

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Adzabwera akunjenjemera ngati mbalame kuchokera ku Ejipito, adzabwera ngati njiŵa kuchokera ku Asiriya. Motero ndidzaŵabwezeranso kwao. Ndikutero Ine Chauta.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Adzabwera akunjenjemera ngati mbalame kuchokera ku Igupto, ngati nkhunda kuchokera ku Asiriya. Ine ndidzawakhazikanso mʼnyumba zawo,” akutero Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 11:11
17 Mawu Ofanana  

Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti Ambuye adzabweza kachiwiri ndi dzanja lake anthu ake otsala ochokera ku Asiriya, ndi ku Ejipito, ndi ku Patirosi, ndi ku Kusi, ndi ku Elamu, ndi ku Sinara, ndi ku Hamati, ndi ku zisumbu za m'nyanja.


Ndani awa amene auluka ngati mtambo, ndi monga nkhunda kumazenera ao?


Ndipo adzadza nadzaimba pa msanje wa Ziyoni, nadzasonkhanira ku zokoma za Yehova, kutirigu, ndi kuvinyo, ndi mafuta, ndi kwa ana a zoweta zazing'ono ndi zazikulu; ndipo moyo wao udzakhala ngati munda wamichera; ndipo sadzakhalanso konse ndi chisoni.


Ndi mitengo yakuthengo idzapereka zobala zao, ndi nthaka idzapereka zipatso zake, ndipo adzakhazikika m'dziko mwao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditadula zomangira goli lao, ndi kuwalanditsa m'manja mwa iwo akuwatumikiritsa.


Ndipo sadzakhalanso chakudya cha amitundu, ndi chilombo chakuthengo sichidzawadyanso; koma adzakhala osatekeseka, opanda wina wakuwaopsa.


Nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga ana a Israele pakati pa amitundu kumene adankako, ndi kuwasokolotsa kumbali zonse, ndi kulowa nao m'dziko mwao;


Ndipo adzakhala m'dziko ndinalipereka kwa Yakobo mtumiki wanga, limene anakhalamo makolo anu, ndipo adzakhala m'mwemo iwo, ndi ana ao, ndi zidzukulu zao kosatha; ndi Davide mtumiki wanga adzakhala mtsogoleri wao kosatha.


atatero ana a Israele adzabwera, nadzafuna Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, nadzafika ndi mantha kwa Yehova, ndi ku ukoma wake masiku otsiriza.


Ndipo Efuremu ali ngati nkhunda yopusa yopanda nzeru; aitanira kwa Ejipito, amuka kwa Asiriya.


Koma m'phiri la Ziyoni mudzakhala opulumuka, ndipo lidzakhala lopatulika; ndi a nyumba ya Yakobo adzakhala nazo zolowa zao.


Ndidzawatenganso kudziko la Ejipito, ndi kuwasonkhanitsa mu Asiriya; ndipo ndidzalowa nao m'dziko la Giliyadi ndi Lebanoni; koma sadzawafikira.


Atero Yehova wa makamu: Taonani, ndidzapulumutsa anthu anga m'dziko la kum'mawa, ndi m'dziko la kumadzulo;


ndipo ndidzabwera nao, nadzakhala m'kati mwa Yerusalemu; ndipo iwo adzakhala anthu anga, nanenanso ndidzakhala Mulungu wao, m'choonadi ndi m'chilungamo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa