Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo

- Zotsatsa -


46 Mau a m'Baibulo Okhudza Ubwana wa Yesu

46 Mau a m'Baibulo Okhudza Ubwana wa Yesu

Ndikudziwa kuti kuyambira ndili mwana, Mulungu anali ndi cholinga chachikulu pa ine. Makolo anga, ndi chikondi chawo chonse, anandiphunzitsa za njira za Ambuye. Ndipo ngakhale ndili mwana, ndinkafunitsitsa kuchita chifuniro cha Atate wanga wakumwamba.

Inonso, muli ndi udindo waukulu kwa ana anu. Muwatsogolere m’njira za Mulungu, kuti akadzakula azitha kuyenda mwamphamvu m’chikhulupiriro. Mulungu amagwiritsa ntchito ana osalakwa kuonetsa ulemerero wake, chifukwa ana samakwiya nthawi yaitali, amapepesana mosavuta, ndipo mitima yawo ndi yoyera.

Yesu anatiuza kuti tikhale ngati ana aang’ono, chifukwa Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu otere. Ndikukhumba kuti ana anu akule akuphunzira Mawu a Mulungu, akupemphera, ndi kutamanda Ambuye ndi nyimbo. Ndikukhumba kuti akule ali olimba mtima, odziwa cholinga chawo choperekedwa ndi Mulungu, ndipo akhale okonzeka kuthana ndi mdima ndi kutsogolera anthu ambiri kwa Khristu.

Masiku ano, Mulungu adzagwiritsa ntchito ana m’njira zodabwitsa. Tiyeni tiwaphunzitse ndi kuwakonzekeretsa nthawi imeneyi yofunika kwambiri.




Yesaya 7:14

Chifukwa chake Ambuye mwini yekha adzakupatsani inu chizindikiro; taonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, nadzamutcha dzina lake Imanuele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:48-49

Ndipo m'mene anamuona Iye, anadabwa; ndipo amake anati kwa Iye, Mwanawe, wachitiranji ife chotero; taona, atate wako ndi ine tinalikufunafuna Iwe ndi kuda nkhawa. Ndipo Iye anati kwa iwo, Kuli bwanji kuti munalikundifunafuna Ine? Simunadziwa kodi kuti kundiyenera Ine ndikhale m'zake za Atate wanga?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:7

Ndipo iye anabala mwana wake wamwamuna woyamba; namkulunga Iye m'nsalu, namgoneka modyera ng'ombe, chifukwa kuti anasowa malo m'nyumba ya alendo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:40

Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 9:6

Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 1:21

Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 1:23

Onani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamutcha dzina lake, Imanuele. Ndilo losandulika, Mulungu nafe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:12

Ndipo ichi ndi chizindikiro kwa inu: Mudzapeza mwana wakhanda wokuta ndi nsalu atagona modyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:80

Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:66

Ndipo onse amene anazimva anazisunga m'mtima mwao, nanena, Nanga mwana uyu adzakhala wotani? Pakuti dzanja la Ambuye linakhala pamodzi ndi iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 1:18-25

Ndipo kubadwa kwake kwa Yesu Khristu kunali kotere: Amai wake Maria anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera. Koma Yosefe, mwamuna wake, anali wolungama, ndiponso sanafune kunyazitsa iye, nayesa m'mtima kumleka iye m'tseri. Abrahamu anabala Isaki; ndi Isaki anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala Yuda ndi abale ake; Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m'kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Maria mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chili cha Mzimu Woyera. Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao. Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti, Onani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamutcha dzina lake, Imanuele. Ndilo losandulika, Mulungu nafe. Ndipo Yosefe anauka tulo take, nachita monga anamuuza mngelo wa Ambuye, nadzitengera yekha mkazi wake; ndipo sanamdziwe iye kufikira atabala mwana wake; namutcha dzina lake Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 1:18

Ndipo kubadwa kwake kwa Yesu Khristu kunali kotere: Amai wake Maria anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:26-38

Ndipo mwezi wachisanu ndi chimodzi mngelo Gabriele anatumidwa ndi Mulungu kunka kumzinda wa ku Galileya dzina lake Nazarete, kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, dzina lake Yosefe, wa fuko la Davide; ndipo dzina lake la namwaliyo ndilo Maria. Ndipo pakulowa mngelo anati kwa iye, Tikuoneni, wochitidwa chisomo, Ambuye ali ndi iwe. Koma iye ananthunthumira ndi mau awa, nasinkhasinkha kulonjera uku nkutani. kuyambira pachiyambi, ndinayesa nkokoma inenso, amene ndinalondalonda mosamalitsa zinthu zonse kuyambira pachiyambi, kulembera kwa iwe tsatanetsatane, Teofilo wabwinotu iwe; Ndipo mngelo anati kwa iye, Usaope, Maria; pakuti wapeza chisomo ndi Mulungu. Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu. Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: ndipo Ambuye Mulungu adzampatsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake: ndipo Iye adzachita ufumu pa banja la Yakobo kunthawi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha. Koma Maria anati kwa mngelo, Ichi chidzachitika bwanji, popeza ine sindidziwa mwamuna? Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu. Ndipo taona, Elizabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna mu ukalamba wake; ndipo mwezi uno uli wachisanu ndi chimodzi wa iye amene ananenedwa wouma. Chifukwa palibe mau amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu. Ndipo Maria anati, Onani, mdzakazi wa Ambuye; kukhale kwa ine monga mwa mau anu. Ndipo mngelo anachoka kwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 9:6-7

Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere. Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:14

Koma Yesu anati, Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine: chifukwa Ufumu wa Kumwamba uli wa totere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:6-7

Ndipo panali pokhala iwo komweko, masiku ake a kubala anakwanira. Ndipo iye anabala mwana wake wamwamuna woyamba; namkulunga Iye m'nsalu, namgoneka modyera ng'ombe, chifukwa kuti anasowa malo m'nyumba ya alendo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:6

Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:39-45

Ndipo Maria ananyamuka masiku amenewa, namuka ndi changu kudziko la mapiri kumzinda wa Yuda; kuti udziwitse zoona zake za mau amene unaphunzira. nalowa m'nyumba ya Zekariya, nalonjera Elizabeti. Ndipo panali pamene Elizabeti anamva kulonjera kwake kwa Maria, mwana wosabadwayo anatsalima m'mimba mwake; ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera; nakweza mau ndi mfuu waukulu, nati, Wodalitsika iwe mwa akazi, ndipo chodalitsika chipatso cha mimba yako. Ndipo ichi chichokera kuti kudza kwa ine, kuti adze kwa ine amake wa Ambuye wanga? Pakuti ona, pamene mau a moni wako analowa m'makutu anga, mwana anatsalima ndi msangalalo m'mimba mwanga. Ndipo wodala ali iye amene anakhulupirira; chifukwa zidzachitidwa zinthu zimene Ambuye analankhula naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:11

Pamene ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana, ndinawerenga ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa chabe zachibwana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:4

Chifukwa chake yense amene adzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:46-55

Ndipo Maria anati, Moyo wanga ulemekeza Ambuye, ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga, chifukwa Iye anayang'anira umphawi wa mdzakazi wake; pakuti taonani, kuyambira tsopano, anthu a mibadwo yonse adzanditchula ine wodala. Chifukwa Iye Wamphamvuyo anandichitira ine zazikulu; ndipo dzina lake lili loyera. Masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali munthu wansembe, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wake wa ana aakazi a fuko la Aroni, dzina lake Elizabeti. Ndipo chifundo chake chifikira anthu a mibadwomibadwo pa iwo amene amuopa Iye. Iye anachita zamphamvu ndi mkono wake; Iye anabalalitsa odzitama ndi mlingaliro wa mtima wao. Iye anatsitsa mafumu pa mipando yao yachifumu, ndipo anakweza aumphawi. Anawakhutitsa anjala ndi zinthu zabwino, ndipo eni chuma anawachotsa opanda kanthu. Anathangatira Israele mnyamata wake, kuti akakumbukire chifundo, (Monga analankhula kwa makolo athu) kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake kunthawi yonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:16-17

Ndipo iwo anadza ndi changu, napeza Maria, ndi Yosefe, ndi mwana wakhanda atagona modyera. Ndipo iwo, m'mene anaona, anadziwitsa anthu za mau analankhulidwa kwa iwo a mwana uyu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 2:1-2

Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu mu Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu, Ndipo iwo poona nyenyeziyo, anakondwera ndi kukondwera kwakukulu. Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Maria amake, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golide ndi lubani ndi mure. Ndipo iwo, pochenjezedwa m'kulota kuti asabwerere kwa Herode, anachoka kupita ku dziko lao panjira ina. Ndipo pamene iwo anachoka, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe m'kulota, nati, Tauka, nutenge kamwanako ndi amake, nuthawire ku Ejipito, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukaononga Iko. Ndipo iye ananyamuka natenga kamwana ndi amake usiku, nachoka kupita ku Ejipito; nakhalabe kumeneko kufikira atamwalira Herode; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri kuti, Ndinaitana Mwana wanga atuluke mu Ejipito. Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta mu Betelehemu ndi ta m'midzi yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo. Pomwepo chinachitidwa chonenedwa ndi Yeremiya mneneri, kuti, Mau anamveka mu Rama, maliro ndi kuchema kwambiri; Rakele wolira ana ake, wosafuna kusangalatsidwa, chifukwa palibe iwo. Koma pakumwalira Herode, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera m'kulota kwa Yosefe mu Ejipito, nati, Ali kuti amene anabadwa mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:1-7

Ndipo kunali masiku aja, kuti lamulo linatuluka kwa Kaisara Augusto kuti dziko lonse lokhalamo anthu lilembedwe; Ndipo mngelo anati kwa iwo, Musaope; pakuti onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa chikondwero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse; pakuti wakubadwirani inu lero, m'mzinda wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Khristu Ambuye. Ndipo ichi ndi chizindikiro kwa inu: Mudzapeza mwana wakhanda wokuta ndi nsalu atagona modyera. Ndipo dzidzidzi panali pamodzi ndi mngeloyo ambirimbiri a gulu la Kumwamba, natamanda Mulungu, nanena, Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao. Ndipo panali, pamene angelo anachokera kwa iwo kunka Kumwamba, abusa anati wina ndi mnzake, Tipitiretu ku Betelehemu, tikaone chinthu ichi chidachitika, chimene Ambuye anatidziwitsira ife. Ndipo iwo anadza ndi changu, napeza Maria, ndi Yosefe, ndi mwana wakhanda atagona modyera. Ndipo iwo, m'mene anaona, anadziwitsa anthu za mau analankhulidwa kwa iwo a mwana uyu. Ndipo anthu onse amene anamva anazizwa ndi zinthu abusa adalankhula nao. Koma Maria anasunga mau awa onse, nawalingalira mumtima mwake. ndiko kulembera koyamba pokhala Kwirinio kazembe wa Siriya. Ndipo abusawo anabwera, nalemekeza ndi kutamanda Mulungu pa zinthu zonse anazimva, naziona, monga kunalankhulidwa kwa iwo. Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula Iye, anamutcha dzina lake Yesu, limene anatchula mngeloyo asanalandiridwe Iye m'mimba. Ndipo pamene anakwanira masiku a kukonza kwao, monga mwa chilamulo cha Mose, iwo anakwera naye kunka ku Yerusalemu, kukamsonyeza Iye kwa Ambuye, (monga mwalembedwa m'chilamulo cha Ambuye, kuti mwamuna aliyense wotsegula pa mimba ya amake adzanenedwa wopatulika wa kwa Ambuye) ndi kukapereka nsembe monga mwanenedwa m'chilamulo cha Ambuye, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri. Ndipo onani, mu Yerusalemu munali munthu, dzina lake Simeoni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopemphera, analikulindira matonthozedwe a Israele; ndipo Mzimu Woyera anali pa iye. Ndipo anamuululira Mzimu Woyera kuti sadzaona imfa, kufikira adzaona Khristu wake wa Ambuye. Ndipo iye analowa ku Kachisi ndi Mzimu: ndipo pamene atate ndi amake analowa ndi kamwanako Yesu, kudzamchitira Iye mwambo wa chilamulo, pomwepo iye anamlandira Iye m'manja mwake, nalemekeza Mulungu, nati, Tsopano, Ambuye, monga mwa mau anu aja, lolani ine, kapolo wanu, ndichoke mumtendere; Ndipo onse anamuka kulembedwa, munthu aliyense kumzinda wake. chifukwa maso anga adaona chipulumutso chanu, chimene munakonza pamaso pa anthu onse, kuunika kukhale chivumbulutso cha kwa anthu a mitundu, ndi ulemerero wa anthu anu Israele. Ndipo atate ndi amake anali kuzizwa ndi zinthu zolankhulidwa za Iye. Ndipo Simeoni anawadalitsa, nati kwa Maria amake, Taona, Uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa Israele; ndipo akhale chizindikiro chakutsutsana nacho; eya, ndipo lupanga lidzakupyoza iwe moyo wako; kuti maganizo a m'mitima yambiri akaululidwe. Ndipo panali Anna, mneneri wamkazi, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere; amene anali wokalamba ndithu, nakhala ndi mwamuna wake, kuyambira pa unamwali wake, zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zake makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sankachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana. Ndipo iye anafikako pa nthawi yomweyo, navomerezanso kutama Mulungu, nalankhula za Iye kwa anthu onse akuyembekeza chiombolo cha Yerusalemu. Ndipo pamene iwo anatha zonse monga mwa chilamulo cha Ambuye, anabwera ku Galileya, kumzinda kwao, ku Nazarete. Ndipo Yosefe yemwe anakwera kuchokera ku Galileya, kumzinda wa Nazarete, kunka ku Yudeya, kumzinda wa Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa iye anali wa banja ndi fuko lake la Davide; Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye. Ndipo atate wake ndi amake akamuka chaka ndi chaka ku Yerusalemu ku Paska. Ndipo pamene Iye anakhala ndi zaka zake khumi ndi ziwiri, anakwera iwo monga machitidwe a chikondwerero; ndipo pakumaliza masiku ake, pakubwera iwo, mnyamatayo Yesu anatsala m'mbuyo ku Yerusalemu. Ndipo atate ndi amake sanadziwe; koma iwo anayesa kuti Iye ali m'chipiringu cha ulendo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi; ndipo anayamba kumfunafuna Iye mwa abale ao ndi mwa anansi ao; ndipo pamene sanampeze, anabwera ku Yerusalemu, namfunafuna Iye. Ndipo pakupita masiku atatu, anampeza Iye mu Kachisi, analikukhala pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsanso mafunso. Ndipo onse amene anamva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake, ndi mayankho ake. Ndipo m'mene anamuona Iye, anadabwa; ndipo amake anati kwa Iye, Mwanawe, wachitiranji ife chotero; taona, atate wako ndi ine tinalikufunafuna Iwe ndi kuda nkhawa. Ndipo Iye anati kwa iwo, Kuli bwanji kuti munalikundifunafuna Ine? Simunadziwa kodi kuti kundiyenera Ine ndikhale m'zake za Atate wanga? kukalembedwa iye mwini pamodzi ndi Maria, wopalidwa naye ubwenzi; ndi uyu anali ndi pakati. Ndipo sanadziwitse mau amene Iye analankhula nao. Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo amake anasunga zinthu izi zonse mumtima mwake. Ndipo Yesu anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu. Ndipo panali pokhala iwo komweko, masiku ake a kubala anakwanira. Ndipo iye anabala mwana wake wamwamuna woyamba; namkulunga Iye m'nsalu, namgoneka modyera ng'ombe, chifukwa kuti anasowa malo m'nyumba ya alendo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:6

Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 2:11

Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Maria amake, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golide ndi lubani ndi mure.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:3

Taonani, ana ndiwo cholowa cha kwa Yehova; chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 2:1-12

Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu mu Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu, Ndipo iwo poona nyenyeziyo, anakondwera ndi kukondwera kwakukulu. Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Maria amake, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golide ndi lubani ndi mure. Ndipo iwo, pochenjezedwa m'kulota kuti asabwerere kwa Herode, anachoka kupita ku dziko lao panjira ina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 9:37

Munthu aliyense adzalandira kamodzi ka tiana totere chifukwa cha dzina langa, alandira Ine; ndipo yense amene akalandira Ine, salandira Ine, koma Iye amene anandituma Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:21

Nthawi yomweyo Iye anakondwera ndi Mzimu Woyera, nati, Ndikuvomerezani Inu, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi, kuti izi munazibisira anzeru ndi ozindikira, ndipo munaziululira ana amakanda; indedi, Atate, pakuti kotero kudakondweretsa pamaso panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:52

Ndipo Yesu anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 2:13-15

Ndipo pamene iwo anachoka, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe m'kulota, nati, Tauka, nutenge kamwanako ndi amake, nuthawire ku Ejipito, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukaononga Iko. Ndipo iye ananyamuka natenga kamwana ndi amake usiku, nachoka kupita ku Ejipito; nakhalabe kumeneko kufikira atamwalira Herode; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri kuti, Ndinaitana Mwana wanga atuluke mu Ejipito.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 2:13

Ndipo pamene iwo anachoka, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe m'kulota, nati, Tauka, nutenge kamwanako ndi amake, nuthawire ku Ejipito, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukaononga Iko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 2:16-18

Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta mu Betelehemu ndi ta m'midzi yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo. Pomwepo chinachitidwa chonenedwa ndi Yeremiya mneneri, kuti, Mau anamveka mu Rama, maliro ndi kuchema kwambiri; Rakele wolira ana ake, wosafuna kusangalatsidwa, chifukwa palibe iwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:41-42

Ndipo atate wake ndi amake akamuka chaka ndi chaka ku Yerusalemu ku Paska. Ndipo pamene Iye anakhala ndi zaka zake khumi ndi ziwiri, anakwera iwo monga machitidwe a chikondwerero;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 2:19-23

Koma pakumwalira Herode, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera m'kulota kwa Yosefe mu Ejipito, nati, Ali kuti amene anabadwa mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye. nati, Tauka, nutenge kamwana ndi amake, nupite kudziko la Israele: chifukwa anafa uja wofuna moyo wake wa kamwanako. Ndipo anauka iye, natenga kamwana ndi amake, nalowa m'dziko la Israele. Koma pakumva iye kuti Arkelao anali mfumu ya Yudeya m'malo mwa atate wake Herode, anachita mantha kupita kumeneko; ndipo pamene anachenjezedwa ndi Mulungu m'kulota, anamuka nalowa kudziko la Galileya, nadza nakhazikika m'mzinda dzina lake Nazarete kuti chikachitidwe chonenedwa ndi aneneri kuti, Adzatchedwa Mnazarayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:21-24

Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula Iye, anamutcha dzina lake Yesu, limene anatchula mngeloyo asanalandiridwe Iye m'mimba. Ndipo pamene anakwanira masiku a kukonza kwao, monga mwa chilamulo cha Mose, iwo anakwera naye kunka ku Yerusalemu, kukamsonyeza Iye kwa Ambuye, (monga mwalembedwa m'chilamulo cha Ambuye, kuti mwamuna aliyense wotsegula pa mimba ya amake adzanenedwa wopatulika wa kwa Ambuye) ndi kukapereka nsembe monga mwanenedwa m'chilamulo cha Ambuye, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:25-35

Ndipo onani, mu Yerusalemu munali munthu, dzina lake Simeoni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopemphera, analikulindira matonthozedwe a Israele; ndipo Mzimu Woyera anali pa iye. Ndipo anamuululira Mzimu Woyera kuti sadzaona imfa, kufikira adzaona Khristu wake wa Ambuye. Ndipo iye analowa ku Kachisi ndi Mzimu: ndipo pamene atate ndi amake analowa ndi kamwanako Yesu, kudzamchitira Iye mwambo wa chilamulo, pomwepo iye anamlandira Iye m'manja mwake, nalemekeza Mulungu, nati, Tsopano, Ambuye, monga mwa mau anu aja, lolani ine, kapolo wanu, ndichoke mumtendere; Ndipo onse anamuka kulembedwa, munthu aliyense kumzinda wake. chifukwa maso anga adaona chipulumutso chanu, chimene munakonza pamaso pa anthu onse, kuunika kukhale chivumbulutso cha kwa anthu a mitundu, ndi ulemerero wa anthu anu Israele. Ndipo atate ndi amake anali kuzizwa ndi zinthu zolankhulidwa za Iye. Ndipo Simeoni anawadalitsa, nati kwa Maria amake, Taona, Uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa Israele; ndipo akhale chizindikiro chakutsutsana nacho; eya, ndipo lupanga lidzakupyoza iwe moyo wako; kuti maganizo a m'mitima yambiri akaululidwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:36-38

Ndipo panali Anna, mneneri wamkazi, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere; amene anali wokalamba ndithu, nakhala ndi mwamuna wake, kuyambira pa unamwali wake, zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zake makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sankachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana. Ndipo iye anafikako pa nthawi yomweyo, navomerezanso kutama Mulungu, nalankhula za Iye kwa anthu onse akuyembekeza chiombolo cha Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:39-40

Ndipo pamene iwo anatha zonse monga mwa chilamulo cha Ambuye, anabwera ku Galileya, kumzinda kwao, ku Nazarete. Ndipo Yosefe yemwe anakwera kuchokera ku Galileya, kumzinda wa Nazarete, kunka ku Yudeya, kumzinda wa Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa iye anali wa banja ndi fuko lake la Davide; Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:41-52

Ndipo atate wake ndi amake akamuka chaka ndi chaka ku Yerusalemu ku Paska. Ndipo pamene Iye anakhala ndi zaka zake khumi ndi ziwiri, anakwera iwo monga machitidwe a chikondwerero; ndipo pakumaliza masiku ake, pakubwera iwo, mnyamatayo Yesu anatsala m'mbuyo ku Yerusalemu. Ndipo atate ndi amake sanadziwe; koma iwo anayesa kuti Iye ali m'chipiringu cha ulendo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi; ndipo anayamba kumfunafuna Iye mwa abale ao ndi mwa anansi ao; ndipo pamene sanampeze, anabwera ku Yerusalemu, namfunafuna Iye. Ndipo pakupita masiku atatu, anampeza Iye mu Kachisi, analikukhala pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsanso mafunso. Ndipo onse amene anamva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake, ndi mayankho ake. Ndipo m'mene anamuona Iye, anadabwa; ndipo amake anati kwa Iye, Mwanawe, wachitiranji ife chotero; taona, atate wako ndi ine tinalikufunafuna Iwe ndi kuda nkhawa. Ndipo Iye anati kwa iwo, Kuli bwanji kuti munalikundifunafuna Ine? Simunadziwa kodi kuti kundiyenera Ine ndikhale m'zake za Atate wanga? kukalembedwa iye mwini pamodzi ndi Maria, wopalidwa naye ubwenzi; ndi uyu anali ndi pakati. Ndipo sanadziwitse mau amene Iye analankhula nao. Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo amake anasunga zinthu izi zonse mumtima mwake. Ndipo Yesu anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 5:2

Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 11:1

Pamene Israele anali mwana, ndinamkonda, ndinaitana mwana wanga ali mu Ejipito.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 72:10-11

Mafumu a ku Tarisisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera nacho chopereka; mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso. Inde mafumu onse adzamgwadira iye, amitundu onse adzamtumikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu, chikopa changa! M'dzina la Yesu, ndikupemphani, kuti ndikhale ndi ubwana wogwirizana ndi chifuniro chanu, ndikukula ndi makhalidwe abwino ndi mfundo zachikhristu. Kukhala ndi ubwana komwe nthawi yanga yambiri ndimakhala m'nyumba mwanu ndi kukhala pafupi ndi inu nthawi zonse, ndi ana anzanga, achinyamata ndi abale m'chikhulcho, komwe pamodzi tingakuimbireni, kukweza manja athu ndi kulambira dzina lanu. Ambuye, ndikhale ndi ubwana komwe pamodzi ndi banja langa ndingaphunzire mawu anu ndi kukutumikirani inu ndi ena, ndi maluso ndi mphatso zomwe mwandipatsa. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa