Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 2:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo pamene iwo anachoka, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe m'kulota, nati, Tauka, nutenge kamwanako ndi amake, nuthawire ku Ejipito, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukaononga Iko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo pamene iwo anachoka, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe m'kulota, nati, Tauka, nutenge kamwanako ndi amake, nuthawire ku Ejipito, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukaononga Iko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Atapita akatswiri a nyenyezi aja, mngelo wa Ambuye adaonekera Yosefe m'maloto. Adamuuza kuti, “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mai wake, uthaŵire ku Ejipito. Ukakhale kumeneko mpaka ndidzakuuze, popeza kuti Herode azidzafunafuna mwanayu kuti amuphe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Atachoka, taonani mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe mʼmaloto nati, “Tadzuka, tenga mwanayo pamodzi ndi amayi ake ndipo muthawire ku Igupto. Mukakhale kumeneko mpaka nditakuwuza pakuti Herode adzafunafuna mwanayo kuti amuphe.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 2:13
29 Mawu Ofanana  

Hadadi uja anathawa, iyeyo ndi a ku Edomu ena, akapolo a atate wake pamodzi naye, kunka ku Ejipito, Hadadiyo akali mwana.


Ku Gibiyoni Yehova anaonekera Solomoni m'kulota usiku, nati Mulungu, Tapempha chimene ndikupatse.


M'kulota, m'masomphenya a usiku, pakuwagwera anthu tulo tatikulu, pogona mwatcheru pakama,


kuti achotse munthu ku chimene akadachita, ndi kubisira munthu kudzikuza kwake;


Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana aamuna onse akabadwa aponyeni m'mtsinje, koma ana aakazi onse alekeni amoyo.


Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m'kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Maria mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chili cha Mzimu Woyera.


Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israele, kufikira Mwana wa Munthu atadza.


Ndipo iwo, pochenjezedwa m'kulota kuti asabwerere kwa Herode, anachoka kupita ku dziko lao panjira ina.


Ndipo iye ananyamuka natenga kamwana ndi amake usiku, nachoka kupita ku Ejipito;


Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta mu Betelehemu ndi ta m'midzi yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo.


Koma pakumva iye kuti Arkelao anali mfumu ya Yudeya m'malo mwa atate wake Herode, anachita mantha kupita kumeneko; ndipo pamene anachenjezedwa ndi Mulungu m'kulota, anamuka nalowa kudziko la Galileya,


Ndipo anati, Kornelio kenturiyoyo, munthu wolungama ndi wakuopa Mulungu, amene mtundu wonse wa Ayuda umchitira umboni, anachenjezedwa ndi mngelo woyera kuti atumize nakuitaneni mumuke kunyumba yake, ndi kumvetsa mau anu.


Ndipo m'mene atachoka mngelo amene adalankhula naye, anaitana anyamata ake awiri, ndi msilikali wopembedza, wa iwo amene amtumikira kosaleka;


Ndipo Petro atatsitsimuka, anati, Tsopano ndidziwa zoona, kuti Ambuye anatuma mngelo wake nandilanditsa ine m'dzanja la Herode, ndi ku chilingiriro chonse cha Ayuda.


Ndipo taonani, mngelo wa Ambuye anaimirirapo, ndipo kuunika kunawala mokhalamo iye; ndipo anakhoma Petro m'nthiti, namuutsa iye, nanena, Tauka msanga. Ndipo maunyolo anagwa kuchoka m'manja mwake.


Ndipo mdindo anafotokozera mauwo kwa Paulo, nati, Oweruza atumiza mau kunena kuti mumuke; tsopanotu tulukani, mukani mumtendere.


Koma mngelo wa Ambuye anatsegula pakhomo pa ndende usiku, nawatulutsa, nati,


Imeneyo inachenjerera fuko lathu, niwachitira choipa makolo athu, niwatayitsa tiana tao, kuti tingakhale ndi moyo.


Ndipo kudzakhala, akaima mapazi a ansembe akusenza likasa la Yehova Ambuye wa dziko lonse, m'madzi a Yordani, adzadulidwa madziwo, ndiwo madzi ochokera kumagwero, nadzaima mulu umodzi.


Ndipo ansembe akulisenza likasa la chipangano la Yehova, anaima pouma pakati pa Yordani, ndi Aisraele onse anaoloka pouma mpaka mtundu wonse unatha kuoloka Yordani.


Pakuti ansembe akusenza likasa anaima pakati pa Yordani, mpaka zitatha zonse Yehova adazilamulira Yoswa anene kwa anthu, monga mwa zonse Mose adalamulira Yoswa; ndipo anthu anafulumira kuoloka.


Ndipo kunali, atakwera ansembe akusenza likasa la chipangano la Yehova, kutuluka pakati pa Yordani, nakwera pamtunda mapazi a ansembe, madzi a mu Yordani anabwera m'njira mwake, nasefuka m'magombe ake onse monga kale.


Ndipo anapatsa mkazi mapiko awiri a chiombankhanga chachikulu, kuti akaulukire kuchipululu, ku mbuto yake, kumene adyetsedwako nthawi, ndi zinthawi, ndi nusu la nthawi, osapenya nkhope ya njoka.


Ndipo mchira wake uguza limodzi la magawo atatu a nyenyezi zam'mwamba, nuziponya padziko. Ndipo chinjoka chinaimirira pamaso pa mkazi akuti abale, kuti, akabala icho chikalikwire mwana wake.


Ndipo mkazi anathawira kuchipululu, kumene ali nayo mbuto yokonzekeratu ndi Mulungu, kuti kumeneko akamdyetse masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa