Koma ife, Yehova ndiye Mulungu wathu, sitinamsiye Iye; ndi ansembe tili nao akutumikira Yehova ana a Aroni, ndi Alevi, m'ntchito mwao,
Yoweli 1:9 - Buku Lopatulika Nsembe yaufa ndi nsembe yothira zalekeka kunyumba ya Yehova; ansembe, atumiki a Yehova, achita maliro. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nsembe yaufa ndi nsembe yothira zalekeka kunyumba ya Yehova; ansembe, atumiki a Yehova, achita maliro. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chopereka cha chakumwa ndi cha chakudya siziperekedwanso ku Nyumba ya Chauta. Ansembe akulira, atumiki a Chauta aja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa sizikuperekedwa ku nyumba ya Yehova. Ansembe akulira, amene amatumikira pamaso pa Yehova. |
Koma ife, Yehova ndiye Mulungu wathu, sitinamsiye Iye; ndi ansembe tili nao akutumikira Yehova ana a Aroni, ndi Alevi, m'ntchito mwao,
Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ake aamuna pamodzi naye, mwa ana a Israele, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni.
Koma inu mudzatchedwa ansembe a Yehova; anthu adzakuyesani inu atumiki a Mulungu wathu; inu mudzadya chuma cha amitundu, nimudzalowa mu ulemerero wao.
Chifukwa cha zimenezi ndilira; diso langa, diso langatu likudza madzi: Pakuti wonditonthoza, wotsitsimutsa moyo wanga, anditalikira; ana anga asungulumwa, pakuti adaniwo apambana.
M'njira za Ziyoni mulira posoweka akudzera msonkhano; pa zipata zake zonse papasuka; ansembe ake onse ausa moyo; anamwali ake asautsidwa; iye mwini namva zowawa.
Sadzatsanulira Yehova nsembe zavinyo; sizidzamkomera Iye nsembe zao; zidzakhala kwa iwo ngati mkate wa achisoni; onse akudyako adzadetsedwa; pakuti mkate wao udzakhala wa njala yao, uwu sudzalowa m'nyumba ya Yehova.
Mudzimangire chiguduli m'chuuno mwanu, nimulire, ansembe inu; bumani otumikira kuguwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m'chiguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu.
Chakudya sichichotsedwa kodi pamaso pathu? Chimwemwe ndi chikondwerero pa nyumba ya Mulungu wathu?
Kaya, kapena adzabwerera, nadzalekerera, ndi kusiya mdalitso pambuyo pake, ndiwo nsembe yaufa ndi nsembe yothira ya Yehova Mulungu wanu.
Ansembe, atumiki a Yehova, alire pakati pa khonde la pakhomo ndi guwa la nsembe, nanene, Alekeni anthu anu, Yehova, musapereka cholowa chanu achitonze, kuti amitundu awalamulire; adzaneneranji mwa anthu, Ali kuti Mulungu wao?