Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 13:10 - Buku Lopatulika

10 Koma ife, Yehova ndiye Mulungu wathu, sitinamsiye Iye; ndi ansembe tili nao akutumikira Yehova ana a Aroni, ndi Alevi, m'ntchito mwao,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Koma ife, Yehova ndiye Mulungu wathu, sitinamsiya Iye; ndi ansembe tili nao akutumikira Yehova ana a Aroni, ndi Alevi, m'ntchito mwao,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Koma kunena za ife, Chauta ndiye Mulungu wathu, ndipo sitidamsiye ai. Tili nawo ansembe, ana a Aaroni, otumikira Chauta, tilinso ndi Alevi amene amatumikira ansembewo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 “Koma kunena za ife, Yehova ndiye Mulungu wathu, ndipo sitinamusiye. Ansembe amene amatumikira Yehova ndi ana a Aaroni ndipo amathandizidwa ndi Alevi.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 13:10
11 Mawu Ofanana  

nafukizira Yehova nsembe zopsereza m'mawa ndi m'mawa, ndi madzulo onse, ndi zonunkhira za fungo lokoma, nakonza mkate woonekera pa gome lopatulika, ndi choikaponyali chagolide ndi nyali zake, ziyake madzulo onse; pakuti tisunga chilangizo cha Yehova Mulungu wathu, koma inu mwamsiya Iye.


Simunapirikitse kodi ansembe a Yehova, ana a Aroni, ndi Alevi, ndi kudziikira ansembe monga amachita anthu a m'maiko ena? Kuti aliyense wakudza kudzipatulira ndi mwanawang'ombe, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, yemweyo ndiye wansembe wa iyo yosati milungu.


Momwemo ndinawayeretsa kuwachotsera achilendo onse, ndi kuikira udikiro ansembe ndi Alevi, yense kuntchito yake;


Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga.


Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa chihema cha mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira chihema cha mboni.


chikhale chikumbutso kwa ana a Israele, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kuchita chofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lake; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose.


pakuti Yehova Mulungu wathu ndi Iye amene anatikweza kutitulutsa m'dziko la Ejipito kunyumba ya ukapolo, nachita zodabwitsa zazikuluzo pamaso pathu, natisunga m'njira monse tidayendamo, ndi pakati pa anthu onse amene tinapita pakati pao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa