Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Maliro 1:4 - Buku Lopatulika

4 M'njira za Ziyoni mulira posoweka akudzera msonkhano; pa zipata zake zonse papasuka; ansembe ake onse ausa moyo; anamwali ake asautsidwa; iye mwini namva zowawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 M'njira za Ziyoni mulira posoweka akudzera msonkhano; pa zipata zake zonse papasuka; ansembe ake onse ausa moyo; anamwali ake asautsidwa; iye mwini namva zowawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Miseu yopita ku Ziyoni yaŵirira, chifukwa palibe wopitako kuti akapembedze pa masiku achikondwerero. Zipata zake zonse zili pululu, ansembe ake akungodandaula. Anamwali ake aja mtima wao ukupweteka, ndithu Ziyoni ali pa masautso oopsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Misewu yopita ku Ziyoni ikulira, chifukwa palibe ndi mmodzi yemwe akubwera ku maphwando ake. Zipata zake zonse zili pululu, ansembe akubuwula. Anamwali ake akulira, ndipo ali mʼmasautso woopsa.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 1:4
19 Mawu Ofanana  

Ndipo zipata zake zidzalira maliro; ndipo iye adzakhala bwinja, nadzakhala pansi.


Mbiri yamveka, taonani ikudza, ndi phokoso lalikulu lituluka m'dziko la kumpoto, likachititse mizinda ya Yuda bwinja, ndi mbuto ya nkhandwe.


Yuda alira, ndipo zipata zake zilefuka, zikhala pansi zovekedwa ndi zakuda; mfuu wa Yerusalemu wakwera.


Ndipo ndidzayesa Yerusalemu miyulu, mbuto ya ankhandwe; ndipo ndidzayesa mizinda ya Yuda bwinja, lopanda wokhalamo.


Iwo anamva kuti ndiusa moyo, palibe wonditonthoza; adani anga onse atha kumva msauko wanga, nakondwera kuti mwatero ndinu; mudzafikitsa tsiku lija mwalitchula, ndipo iwowo adzanga ine.


Anyamata ananyamula mphero, ana nakhumudwa posenza nkhuni.


Akulu adatha kuzipata, anyamata naleka nyimbo zao.


Ndipo ndidzamlanga chifukwa cha masiku a Abaala amene anawafukizira, navala mphete za m'mphuno, ndi zokometsera zake, natsata omkonda, nandiiwala Ine, ati Yehova.


Popeza ndidzatumiza chilombo chakuthengo pakati pa inu, ndipo chidzalanda ana anu, ndi kuononga zoweta zanu ndipo chidzachepetsa inu kuti mukhale pang'ono; ndi njira zanu zidzakhala zakufa.


Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati munda chifukwa cha inu, ndi mu Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m'nkhalango.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa