Yoweli 1:13 - Buku Lopatulika13 Mudzimangire chiguduli m'chuuno mwanu, nimulire, ansembe inu; bumani otumikira kuguwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m'chiguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Mudzimangire chiguduli m'chuuno mwanu, nimulire, ansembe inu; bumani otumikira kuguwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m'chiguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Inu ansembe, valani ziguduli mudzigunde pa chifuwa chifukwa cha chisoni. Lirani, inu otumikira ku guwa. Tiyeni, mufunde ziguduli usiku wonse, inu atumiki a Mulungu wanga. Pakuti chopereka cha chakudya ndi chakumwa sizidzaonekanso ku Nyumba ya Mulungu wanu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Inu ansembe, valani ziguduli ndipo lirani; lirani mofuwula, inu amene mumatumikira pa guwa lansembe. Bwerani, fundani ziguduli usiku wonse, inu amene mumatumikira pamaso pa Mulungu wanga; pakuti chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa sizikupezekanso mʼnyumba ya Mulungu wanu. Onani mutuwo |