Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoweli 1:14 - Buku Lopatulika

14 Patulani tsiku losala, lalikirani misonkhano yoletsa, sonkhanitsani akuluakulu, ndi onse okhala m'dziko, kunyumba ya Yehova Mulungu wanu; nimufuulire kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Patulani tsiku losala, lalikirani masonkhano oletsa, sonkhanitsani akuluakulu, ndi onse okhala m'dziko, kunyumba ya Yehova Mulungu wanu; nimufuulire kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Lamulani kuti anthu asale zakudya. Itanitsani msonkhano waulemu. Akulu ndi onse okhala m'dziko asonkhane ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu, ndipo iwowo alire kwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Lengezani tsiku lopatulika losala zakudya, itanani msonkhano wopatulika. Sonkhanitsani akuluakulu ndi anthu onse okhala mʼdziko ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu ndipo alirire Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Yoweli 1:14
15 Mawu Ofanana  

Nati Yehu, Lalikirani msonkhano wopatulika wa Baala. Naulalikira.


Ndipo Ayuda onse anakhala chilili pamaso pa Yehova, pamodzi ndi makanda ao, akazi ao, ndi ana ao.


Anawerenganso m'buku la chilamulo cha Mulungu tsiku ndi tsiku, kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lotsiriza. Nachita chikondwerero masiku asanu ndi awiri; ndi tsiku lachisanu ndi chitatu ndilo msonkhano woletsa, monga mwa malemba.


Muka, sonkhanitsa Ayuda onse opezeka mu Susa, nimundisalire, osadya osamwa masiku atatu, usiku ndi usana, ine ndemwe ndi anamwali anga tidzasala momwemo, ndipo motero ndidzalowa kwa mfumu, ndiko kosalingana ndi lamulo; ndikaonongeka tsono ndionongeke.


Yuda alira, ndipo zipata zake zilefuka, zikhala pansi zovekedwa ndi zakuda; mfuu wa Yerusalemu wakwera.


Ndipo panali chaka chachisanu cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mwezi wachisanu ndi chinai, anthu onse a mu Yerusalemu, ndi anthu onse ochokera m'mizinda ya Yuda kudza ku Yerusalemu, analalikira kusala kudya pamaso pa Yehova.


Imvani ichi, akuluakulu inu, nimutchere khutu, inu nonse okhala m'dziko. Chachitika ichi masiku anu kodi, kapena masiku a makolo anu?


Masiku asanu ndi awiri mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; tsiku lachisanu ndi chitatu mukhale nao msonkhano wopatulika; ndipo mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; ndilo lotsirizira; musamagwira ntchito ya masiku ena.


Ndipo anthu a Ninive anakhulupirira Mulungu, nalalikira chosala, navala chiguduli, kuyambira wamkulu kufikira wamng'ono wa iwowa.


koma zifundidwe ndi chiguduli munthu ndi nyama, ndipo zifuulire kolimba kwa Mulungu; ndipo abwere yense kuleka njira yake yoipa, ndi chiwawa chili m'manja mwake.


Dzisanthuleni, inde santhulani; inu mtundu wosakhumba kanthu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa