Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoweli 1:15 - Buku Lopatulika

15 Kalanga ine, tsikuli! Pakuti layandikira tsiku la Yehova, lidzafika ngati chionongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Kalanga ine, tsikuli! Pakuti layandikira tsiku la Yehova, lidzafika ngati chionongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Kalanga ine! Tsiku loopsa layandikira, tsiku la Chauta, likubwera ndi chiwonongeko chochokera kwa Mphambe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Kalanga ine tsikulo! Pakuti tsiku la Yehova layandikira; lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuzonse.

Onani mutuwo Koperani




Yoweli 1:15
18 Mawu Ofanana  

Ambuye adzamseka, popeza apenya kuti tsiku lake likudza.


Kalanga ine! Pakuti nlalikulu tsikulo, palibe lina lotere; ndi nthawi ya msauko wa Yakobo; koma adzapulumuka m'menemo.


Pakuti tsikulo ndi la Ambuye, Yehova wa makamu, tsiku lakubweza chilango, kuti abwezere chilango adani ake; ndipo lupanga lidzadya, lidzakhuta, nilidzamwetsa mwazi wao; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, ali ndi nsembe m'dziko la kumpoto pamtsinje wa Yufurate.


Pakuti layandikira tsiku, layandikira tsiku la Yehova, tsiku lamitambo, ndiyo nyengo ya amitundu.


ndipo Yehova amveketsa mau ake pamaso pa khamu lake la nkhondo; pakuti a m'chigono mwake ndi ambirimbiri; pakuti Iye wakuchita mau ake ndiye wamphamvu ndithu; pakuti tsiku la Yehova ndi lalikulu ndi loopsa ndithu; akhoza kupirira nalo ndani?


Dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsa.


Aunyinji, aunyinji m'chigwa chotsirizira mlandu! Pakuti layandikira tsiku la Yehova m'chigwa chotsirizira mlandu.


Pakuti tsiku la Yehova layandikira amitundu onse; monga unachita iwe, momwemo adzakuchitira; chochita iwe chidzakubwerera pamutu pako.


Khala chete pamaso pa Ambuye Yehova; pakuti tsiku la Yehova liyandikira; pakuti Yehova wakonzeratu nsembe, anapatula oitanidwa ake.


Musaipidwe wina ndi mnzake, abale, kuti mungaweruzidwe. Taonani, woweruza aima pakhomo.


chifukwa lafika tsiku lalikulu la mkwiyo wao, ndipo akhoza kuima ndani?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa