Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoweli 1:12 - Buku Lopatulika

12 Mpesa wauma, mkuyu wafota, mtengo wa mkangaza ndi kanjedza ndi muula, inde mitengo yonse yakuthengo yafota; pakuti chimwemwe chathera ana a anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Mpesa wauma, mkuyu wafota, mtengo wa mkangaza ndi kanjedza ndi muula, inde mitengo yonse ya kuthengo yafota; pakuti chimwemwe chathera ana a anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Mpesa wauma, mkuyu wafota. Mkangaza, kanjedza, mitengo ya apulosi ndi mitengo yonse ya m'dziko yaumiratu. Choncho chikondwerero cha anthu chatheratu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Mpesa wauma ndipo mtengo wamkuyu wafota; makangadza, kanjedza ndi mitengo ya apulosi, mitengo yonse ya mʼmunda yauma. Ndithudi chimwemwe cha anthu chatheratu.

Onani mutuwo Koperani




Yoweli 1:12
19 Mawu Ofanana  

Mwapatsa chimwemwe mumtima mwanga, chakuposa chao m'nyengo yakuchuluka dzinthu zao ndi vinyo wao.


Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa; adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni.


Ngati maula pakati pa mitengo ya m'nkhalango, momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana aamuna. Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wake, zipatso zake zinatsekemera m'kamwa mwanga.


Mphukira zako ndi munda wamakangaza, ndi zipatso zofunika, bonongwe ndi narido.


Ndipo chikondwerero ndi msangalalo zachotsedwa m'munda wopatsa zipatso; ndi m'minda ya mipesa simudzakhala kuimba, ngakhale phokoso losangalala; palibe woponda adzaponda vinyo m'moponderamo; ndaleketsa mfuu wa masika amphesa.


Muli mfuu m'makwalala chifukwa cha vinyo; kukondwa konse kwadetsedwa, kusangalala kwa dziko kwatha.


Vinyo watsopano alira, mpesa ulefuka, mitima yonse yokondwa iusa moyo.


Inu mwachulukitsa mtundu, inu mwaenjezera kukondwa kwao; iwo akondwa pamaso panu monga akondwera m'masika, monga anthu akondwa pogawana zofunkha.


Mau amveka kuchokera ku Horonaimu, kufunkha ndi kuononga kwakukulu!


Ndipo kusekera ndi kukondwa kwachotsedwa, kumunda wobala ndi kudziko la Mowabu; ndipo ndaletsa vinyo pa zoponderamo; sadzaponda ndi kufuula; kufuula sikudzakhala kufuula.


M'munda mwaonongeka, nthaka ilira; pakuti tirigu waonongeka, vinyo watsopano wamwelera, mafuta akudza pang'onong'ono.


Chakudya sichichotsedwa kodi pamaso pathu? Chimwemwe ndi chikondwerero pa nyumba ya Mulungu wathu?


Koma Mulungu anauikira mphanzi pakucha m'mawa mwake, ndiyo inadya msatsi, nufota.


Kodi mbeu ikali m'nkhokwe? Ngakhale mpesa, ndi mkuyu, ndi khangaza ndi azitona sizinabale; kuyambira lero lino ndidzakudalitsani.


Ndipo ndidzadzudzula zolusa chifukwa cha inu, kuti zisakuonongereni zipatso za nthaka yanu; ngakhale mpesa wanu sudzayoyoka zipatso zake, zosacha m'munda, ati Yehova wa makamu.


Ndipo anadza ku chigwa cha Esikolo, nachekako tsango limodzi la mphesa, nalisenza awiri mopika; anabwera nazonso makangaza ndi nkhuyu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa