Anayamba iye kupeza mbale wake yekha Simoni, nanena naye, Tapeza ife Mesiya (ndiko kusandulika Khristu).
Yohane 7:41 - Buku Lopatulika Ena ananena, Uyu ndi Khristu. Koma ena ananena, Kodi Khristu adza kutuluka mu Galileya? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ena ananena, Uyu ndi Khristu. Koma ena ananena, Kodi Khristu adza kutuluka m'Galileya? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ena ankanena kuti, “Ameneyu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja.” Koma ena ankanena kuti, “Kodi Mpulumutsiyo nkuchokera ku Galileya ngati? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ena anati, “Iye ndiye Khristu.” Komanso ena anafunsa kuti, “Kodi Khristu angachokere bwanji ku Galileya? |
Anayamba iye kupeza mbale wake yekha Simoni, nanena naye, Tapeza ife Mesiya (ndiko kusandulika Khristu).
Natanaele anati kwa iye, Ku Nazarete nkutha kuchokera kanthu kabwino kodi? Filipo ananena naye, Tiye ukaone.
Mkazi ananena ndi Iye, Ndidziwa kuti Mesiya adza (wotchedwa Khristu): akadzadza Iyeyu, adzatiuza zonse.
Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu zilizonse ndinazichita: ameneyu sali Khristu nanga?
ndipo ananena kwa mkazi, kuti, Tsopano sitikhulupirira chifukwa cha kulankhula kwako: pakuti tamva tokha, ndipo tidziwa kuti Mpulumutsi wa dziko lapansi ndi Iyeyu ndithu.
Koma ameneyo tidziwa uko achokera: koma Khristu pamene akadzadza, palibe mmodzi adzadziwa uko achokera.
Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira Iye; ndipo ananena, Pamene Khristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo?
Anayankha nati kwa iye, Kodi iwenso uli wotuluka mu Galileya? Santhula, nuone kuti mu Galileya sanauke mneneri.