Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 7:52 - Buku Lopatulika

52 Anayankha nati kwa iye, Kodi iwenso uli wotuluka mu Galileya? Santhula, nuone kuti mu Galileya sanauke mneneri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

52 Anayankha nati kwa iye, Kodi iwenso uli wotuluka m'Galileya? Santhula, nuone kuti m'Galileya sanauke mneneri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

52 Iwo adati, “Kani iwenso ndiwe wa ku Galileya? Kafunefune m'Malembo ndipo udzaona kuti palibe mneneri wochokera ku Galileya.” [

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

52 Iwo anayankha kuti, “Kodi ndiwenso wochokera ku Galileya? Tayangʼananso, ndipo udzapeza kuti mneneri sachokera ku Galileya.”

Onani mutuwo Koperani




Yohane 7:52
11 Mawu Ofanana  

Ndipo anati iwo, Baima; natinso, Uyu anadza kuno kukhala ngati mlendo, ndipo afuna kutilamulira; tsopano tidzakuchitira iwe koipa koposa iwo. Ndipo iwo anamkakamiza munthuyo Loti ndithu, nayandikira kuti aswe chitseko.


Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenana anasendera, napanda Mikaya patsaya, nati, Mzimu wa Yehova wandichokera bwanji, kulankhula ndi iwe?


Koma anati, Wakuika iwe ndani ukhale mkulu ndi woweruza wathu? Kuteroku ukuti undiphe, monga unamupha Mwejipito? Ndipo Mose anachita mantha, nanena, Ndithu chinthuchi chadziwika.


Natanaele anati kwa iye, Ku Nazarete nkutha kuchokera kanthu kabwino kodi? Filipo ananena naye, Tiye ukaone.


Musanthula m'malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nao moyo wosatha; ndipo akundichitira Ine umboni ndi iwo omwewo;


Ena ananena, Uyu ndi Khristu. Koma ena ananena, Kodi Khristu adza kutuluka mu Galileya?


Ndipo anamuka munthu yense kunyumba yake.


Anayankha nati kwa iye, Wabadwa iwe konse m'zoipa, ndipo iwe utiphunzitse ife kodi? Ndipo anamtaya kunja.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa