Yohane 7:10 - Buku Lopatulika Koma pamene abale ake adakwera kunka kuchikondwerero, pomwepo Iyenso anakwera, si poonekera, koma monga mobisalika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma pamene abale ake adakwera kunka kuchikondwerero, pomwepo Iyenso anakwera, si poonekera, koma monga mobisalika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma abale ake atapita ku chikondwerero cha Misasa chija, Yesu nayenso adapitako. Sadapite moonekera, koma mobisika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Komabe, abale ake atanyamuka kupita kuphwando, Iye anapitanso, osati moonekera, koma mseri. |
kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali m'kati mwamtima mwanga.
Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.
Pamene Iye anali chilankhulire ndi makamu, onani, amake ndi abale ake anaima panja, nafuna kulankhula naye.
Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye.
Chifukwa chake Yesu sanayendeyendenso poonekera mwa Ayuda, koma anachokapo kunka kudziko loyandikira chipululu, kumudzi dzina lake Efuremu; nakhala komweko pamodzi ndi ophunzira ake.
Chifukwa chake abale ake anati kwa Iye, Chokani pano, mumuke ku Yudeya, kuti ophunzira anunso akapenye ntchito zanu zimene muchita.
koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu anatuma Mwana wake, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo,