Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Amosi 5:13 - Buku Lopatulika

13 Chifukwa chake wochenjerayo akhala chete nthawi yomweyo; pakuti ndiyo nthawi yoipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Chifukwa chake wochenjerayo akhala chete nthawi yomweyo; pakuti ndiyo nthawi yoipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Nchifukwa chake pa nthaŵi yotere munthu wanzeru salankhulapo kanthu, chifukwa ndi nthaŵi yoipa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Nʼchifukwa chake pa nthawi yotere munthu wanzeru sayankhulapo kanthu, popeza ndi nthawi yoyipa.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 5:13
17 Mawu Ofanana  

Koma anthuwo anakhala chete osamyankha mau; pakuti lamulo la mfumu ndilo kuti, Musamuyankha.


Kodi ndidzangolindira popeza sanena iwo, popeza akhala duu osayankhanso?


Inde ndikunga munthu wosamva, ndipo m'kamwa mwanga mulibe makani.


mphindi yakung'amba ndi mphindi yakusoka; mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula;


Pakuti munthu sadziwatu mphindi yake; monga nsomba zigwidwa mu ukonde woipa, ndi mbalame zikodwa mumsampha, momwemo ana a anthu amagwidwa ndi nthawi ya tsoka, ngati msampha umene uwagwera modzidzimuka.


Koma iwo anakhala chete, osamuyankha mau, pakuti mfumu inawalamulira kuti, Musamuyankhe.


Ndipo iwo anati kwa iye, Hezekiya atere, Tsiku lalero ndilo tsiku la vuto, ndi lakudzudzula ndi chitonzo; pakuti nthawi yake yakubala ana yafika, ndipo palibe mphamvu yobalira.


Koma munthu asatsutsane ndi mnzake, kapena kudzudzula mnzake; popeza anthu ako ndiwo akunga otsutsana ndi wansembe.


Ndipo mbale wake wa munthu akamnyamula, ndiye womtentha, kutulutsa mafupa m'nyumba, nakati kwa iye ali m'kati mwa nyumbamo, Atsala wina nawe kodi? Nakati Iai; pamenepo adzati, Khala chete; pakuti sitingatchule dzina la Yehova.


Chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndilingirira choipa pa banja ili, chimene simudzachotsako makosi anu, kapena kuyenda modzikuza inu; pakuti nyengo iyi ndi yoipa.


Ndinamva, ndi m'mimba mwanga munabwadamuka, milomo yanga inanthunthumira pamau, m'mafupa mwanga mudalowa chivundi, ndipo ndinanjenjemera m'malo mwanga; kuti ndipumule tsiku lamsauko, pamene akwerera anthu kuti ayambane nao ndi makamu.


Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika.


Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthawi zowawitsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa