Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israele, kufikira Mwana wa Munthu atadza.
Yohane 4:3 - Buku Lopatulika anachokera ku Yudeya, namukanso ku Galileya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 anachokera ku Yudeya, namukanso ku Galileya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Yesu adadziŵa kuti Afarisi azimva zimenezi, adachokako ku Yudeya napitanso ku Galileya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anachoka ku Yudeya ndi kubwereranso ku Galileya. |
Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israele, kufikira Mwana wa Munthu atadza.
Ndipo Yesu anachokako pamodzi ndi ophunzira ake nanka kunyanja: ndipo linamtsata khamu lalikulu la a ku Galileya, ndi a ku Yudeya,
M'mawa mwake anafuna kutuluka kunka ku Galileya, napeza Filipo. Ndipo Yesu ananena naye, Tsata Ine.
Ndipo anachoka kunkanso tsidya lija la Yordani, kumalo kumene kunali Yohane analikubatiza poyamba paja; ndipo anakhala komweko.
Chifukwa chake Yesu sanayendeyendenso poonekera mwa Ayuda, koma anachokapo kunka kudziko loyandikira chipululu, kumudzi dzina lake Efuremu; nakhala komweko pamodzi ndi ophunzira ake.
Chiyambi ichi cha zizindikiro zake Yesu anachita mu Kana wa mu Galileya naonetsera ulemerero wake; ndipo ophunzira ake anakhulupirira Iye.
Zitapita izi anadza Yesu ndi ophunzira ake kudziko la Yudeya; ndipo pamenepo anatsotsa nao pamodzi, nabatiza.
Chimene anachiona nachimva, achita umboni wa ichi chomwe; ndipo kulibe munthu alandira umboni wake.
Iyeyu, pamene anamva kuti Yesu wachokera ku Yudeya nafika ku Galileya, ananka kwa Iye, nampempha kuti atsike kukachiritsa mwana wake; pakuti anali pafupi imfa.
Ndipo zitapita izi Yesu anayendayenda mu Galileya; pakuti sanafune kuyendayenda mu Yudeya, chifukwa Ayuda anafuna kumupha Iye.