Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Obadiya 1:5 - Buku Lopatulika

Akakudzera akuba, kapena mbala usiku, (Ha! Waonongeka) sadzaba mpaka adzakhuta kodi? Akakudzera akutchera mphesa sadzasiya khunkha kodi?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Akakudzera akuba, kapena mbala usiku, (Ha! Waonongeka) sadzaba mpaka adzakhuta kodi? Akakudzera akutchera mphesa sadzasiya khunkha kodi?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

“Akuba akabwera usiku, amangotengako zimene akufuna. Okolola akamathyola zipatso, amasiyako zina. Koma inuyo adani anu akupululani kotheratu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Anthu akuba akanabwera kwa iwe, kapena anthu olanda zinthu akanafika usiku, aa, tsoka lanji limene likukudikira iwe! Kodi akanangotengako zimene akuzifuna zokha? Ngati anthu othyola mphesa akanafika, kodi akanakusiyiraniko mphesa pangʼono pokha?

Onani mutuwo



Obadiya 1:5
13 Mawu Ofanana  

Ulemerero wako, Israele, unaphedwa pa misanje yako. Ha! Adagwa amphamvu!


Wagwadi kuchokera kumwamba, iwe nthanda, mwana wa mbandakucha! Wagwetsedwa pansi, iwe wolefula amitundu!


Koma mudzasiyidwa m'menemo khunkha, monga ngati kugwedeza kwake kwa mtengo wa azitona, zipatso ziwiri pena zitatu m'nsonga ya nthambi yosomphoka, zinai pena zisanu m'nthambi za kunthemba, za mtengo wobalitsa, ati Yehova, Mulungu wa Israele.


Chifukwa chake padzakhala chotero pakati padziko mwa anthu, ngati kugwedeza kwa mtengo wa azitona, ngati khunkha la mphesa, pakutha masika ake.


Akafika kwa inu akutchera mphesa, sadzasiya mphesa zokunkha? Akafika usiku akuba, adzaononga mpaka kutha?


Nyundo ya dziko lonse yaduka ndi kuthyoka! Babiloni wasanduka bwinja pakati pa amitundu!


Yehova wa makamu atero, Adzakunkha otsalira a Israele monga mpesa; bweza dzanja lako monga wakutchera mphesa m'madengu ake.


Ha! Mzindawo unadzala anthu, ukhalatu pa wokha! Ukunga mkazi wamasiye! Waukuluwo mwa amitundu, kalonga wamkazi m'madera a dziko wasanduka wolamba!


Ndipo amuna anu amphamvu adzatenga nkhawa, Temani iwe, kuti onse aonongeke m'phiri la Edomu, ndi kuphedwa.


Kalanga ine! Pakuti ndikunga atapulula zipatso za m'mwamvu, atakunkha m'munda wampesa; palibe mphesa zakudya; moyo wanga ukhumba nkhuyu yoyamba kupsa.


Uwu ndi mzinda wosekererawo unakhala wosasamalira, unanena m'mtima mwake, Ine ndine, ndi wopanda ine palibe wina; ha! Wasanduka bwinja, mogonera nyama zakuthengo! Yense wakuupitirira adzatsonya mtsonyo, ndi kupukusa mutu.


Mutatchera m'munda wanu wampesa, musakunkha pambuyo panu; zikhale za mlendo, za mwana wamasiye, ndi za mkazi wamasiye.


chifukwa chakuopa chizunzo chake, nanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukuluwo, Babiloni, mzinda wolimba! Pakuti mu ora limodzi chafika chiweruziro chanu.