Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Obadiya 1:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo amuna anu amphamvu adzatenga nkhawa, Temani iwe, kuti onse aonongeke m'phiri la Edomu, ndi kuphedwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo amuna anu amphamvu adzatenga nkhawa, Temani iwe, kuti onse aonongeke m'phiri la Edomu, ndi kuphedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ngwazi za ku Temani zidzachita mantha, ankhondo onse adzaphedwa ku mapiri a Esau.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ankhondo ako, iwe Temani, adzachita mantha, ndipo aliyense amene ali mʼphiri la Esau adzaphedwa pa nkhondo.

Onani mutuwo Koperani




Obadiya 1:9
19 Mawu Ofanana  

Ndipo ana aamuna a Elifazi ndiwo Temani, Omara, Zefo ndi Gatamu, ndi Kenazi.


Namwalira Yobabu; ndi Husamu wa ku dziko la Atemani anakhala mfumu m'malo mwake.


Atamva tsono mabwenzi atatu a Yobu za choipa ichi chonse chidamgwera, anadza, yense kuchokera kwao, Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, napangana kudzafika kumlirira ndi kumsangalatsa.


Chifukwa chake tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Edomu; ndi zimene walingalirira okhala mu Temani, ndithu adzawakoka, ana aang'ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao.


Taonani, adzafika nadzauluka ngati chiombankhanga, adzatambasulira Bozira mapiko ake, ndipo tsiku lomwemo mtima wa anthu amphamvu a Edomu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.


Za Edomu. Yehova wa makamu atero: Kodi mu Temani mulibenso nzeru? Kodi uphungu wawathera akuchenjera? Kodi nseru zao zatha psiti?


chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ndidzatambasulira Edomu dzanja langa, ndi kulilikhira munthu ndi nyama, ndi kulisandutsa labwinja; kuyambira ku Temani mpaka Dedani adzagwa ndi lupanga.


koma ndidzatumiza moto pa Temani, udzanyeketsa nyumba zachifumu za Bozira.


ndi wolimba mtima mwa ngwazi adzathawa wamaliseche tsiku lomwelo, ati Yehova.


Ndipo apulumutsi adzakwera paphiri la Ziyoni kuweruza phiri la Esau; ndipo ufumu udzakhala wake wa Yehova.


Akakudzera akuba, kapena mbala usiku, (Ha! Waonongeka) sadzaba mpaka adzakhuta kodi? Akakudzera akutchera mphesa sadzasiya khunkha kodi?


Taona, anthu ako m'kati mwako akunga akazi, zipata za dziko lako zatsegulidwira adani ako papakulu; moto watha mipingiridzo yako.


Mulungu anafuma ku Temani, ndi Woyerayo kuphiri la Parani. Ulemerero wake unaphimba miyamba, ndi dziko lapansi linadzala ndi kumlemekeza.


musalimbana nao; popeza sindikupatsakoni dziko lao, pangakhale popondapo phazi lanu ai; pakuti ndapatsa Esau phiri la Seiri likhale lakelake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa