Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Obadiya 1:10 - Buku Lopatulika

10 Chifukwa cha chiwawa unamchitira mphwako Yakobo, udzakutidwa ndi manyazi, nudzaonongeka kunthawi yonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Chifukwa cha chiwawa unamchitira mphwako Yakobo, udzakutidwa ndi manyazi, nudzaonongeka kunthawi yonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 “Aedomu inu, chifukwa cha zankhanza zimene mudachita abale anu, zidzukulu za Yakobe, adzakuchititsani manyazi ndi kukuwonongani mpaka muyaya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Chifukwa cha nkhanza zimene unachitira mʼbale wako Yakobo, udzakhala wamanyazi; adzakuwononga mpaka muyaya.

Onani mutuwo Koperani




Obadiya 1:10
30 Mawu Ofanana  

Yakobo ndipo anati kwa Rebeka amake, Taonani, Esau mkulu wanga ndiye munthu waubweya, ine ndine munthu wosalala.


Ndipo Esau anamuda Yakobo chifukwa cha mdalitso umene atate wake anamdalitsa nao: ndipo Esau anati m'mtima mwake, Masiku a maliro a atate wanga ayandikira; pamenepo ndipo ndidzamupha mphwanga Yakobo.


Pakuti Aedomu anadzanso, nakantha Yuda, natenga andende.


Otsutsana nane avale manyazi, nadzikute nacho chisokonezo chao ngati ndi chofunda.


Ndidzawaveka adani ake ndi manyazi; koma pa iyeyu korona wake adzamveka.


Yehova, kumbukirani ana a Edomu tsiku la Yerusalemu; amene adati, Gamulani, gamulani, kufikira maziko ake.


Pakuti ndalola chotonza chifukwa cha Inu, chimpepulo chakuta nkhope yanga.


Munafupikitsa masiku a mnyamata wake; munamkuta nao manyazi.


Madalitso ali pamutu pa wolungama; koma m'kamwa mwa oipa mubisa chiwawa.


Wochitira chiphwete aumphawi atonza Mlengi; wokondwera ndi tsoka sadzapulumuka chilango.


Atero Yehova ponenera anansi anga onse oipa, amene akhudza cholowa chimene ndalowetsamo anthu anga Israele; taonani, ndidzazula iwo m'dziko lao, ndipo ndidzazula nyumba ya Yuda pakati pao.


Tigone m'manyazi athu, kunyala kwathu kutifunde ife; pakuti tamchimwira Yehova Mulungu wathu, ife ndi makolo athu, kuyambira ubwana wathu kufikira lero lomwe; ndipo sitidamvere mau a Yehova Mulungu wathu.


Pakuti ndalumbira, Pali Ine ati Yehova, kuti Bozira adzakhala chizizwitso, chitonzo, chopasuka, ndi chitemberero; ndipo mizinda yake yonse idzakhala yopasuka chipasukire.


Tili ndi manyazi, chifukwa tamva mnyozo; manyazi aphimba nkhope zathu; pakuti alendo alowa m'malo opatulika a nyumba ya Yehova.


kondwera nusangalale, mwana wamkazi wa Edomu, wokhala m'dziko la Uzi; chikho chidzapita ngakhale mwa iwenso; udzaledzera ndi kuvula zako.


Mphulupulu yako yatha, mwana wamkazi wa Ziyoni, Yehova sadzakutenganso ndende; koma adzazonda mphulupulu yako, mwana wa mkazi wa Edomu, nadzavumbulutsa zochimwa zako.


Ndidzakusandutsa mabwinja osatha; ndi m'mizinda mwako simudzakhalanso anthu; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


Ndipo adzadzimangira m'chuuno ndi ziguduli, ndi zoopsetsa zidzawaphimba, ndi nkhope zonse zidzachita manyazi, ndi mitu yao yonse idzachita dazi.


Ejipito adzasanduka bwinja, ndi Edomu adzasanduka chipululu chopanda kanthu, chifukwa cha chiwawachi anawachitira ana a Yuda; popeza anakhetsa mwazi wosachimwa m'dziko lao.


Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Edomu, kapena zinani, sindidzabweza kulanga kwake; popeza analondola mphwake ndi lupanga, nafetsa chifundo chake chonse, ndi mkwiyo wake unang'amba ching'ambire nasunga mkwiyo wake chisungire;


Pamenepo mdani wanga adzachiona, ndi manyazi adzamkuta iye amene adati kwa ine, Ali kuti Yehova Mulungu wako? Maso anga adzamuona; tsopano adzampondereza ngati thope la m'miseu.


Musamanyansidwa naye Mwedomu, popeza ndiye mbale wanu; musamanyansidwa naye Mwejipito, popeza munali alendo m'dziko lake.


Ana obadwa nao a mbadwo wachitatu alowe m'msonkhano wa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa