Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Maliro 1:1 - Buku Lopatulika

1 Ha! Mzindawo unadzala anthu, ukhalatu pa wokha! Ukunga mkazi wamasiye! Waukuluwo mwa amitundu, kalonga wamkazi m'madera a dziko wasanduka wolamba!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ha! Mudziwo unadzala anthu, ukhalatu pa wokha! Ukunga mkazi wamasiye! Waukuluwo mwa amitundu, kalonga wamkazi m'madera a dziko wasanduka wolamba!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ha! Mzinda wa Yerusalemu wakhala wokhawokha, m'menemo kale udaali wodzaza ndi anthu! Kale unali wotchuka pakati pa mitundu ya anthu, koma tsopano wasanduka ngati mkazi wamasiye. Kale unali mzinda wolemekezeka koposa mizinda ina, koma tsopano wasanduka kapolo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Haa! Mzinda uja wasiyidwa wokhawokha, umene kale unali wodzaza ndi anthu! Kale unali wotchuka pakati pa mitundu ya anthu! Tsopano wasanduka ngati mkazi wamasiye. Kale unali mfumukazi ya onse pa dziko lapansi, tsopano wasanduka kapolo.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 1:1
38 Mawu Ofanana  

Ndipo Solomoni analamulira maiko onse, kuyambira ku Yufurate kufikira ku dziko la Afilisti ndi ku malire a Ejipito; anthu anabwera nayo mitulo namtumikira Solomoni masiku onse a moyo wake.


Ndipo Farao Neko anammanga mu Ribula, m'dziko la Hamati; kuti asachite ufumu mu Yerusalemu; nasonkhetsa dzikoli msonkho wa matalente zana limodzi la siliva, ndi talente limodzi la golide.


Ndipo Yehoyakimu anapereka siliva ndi golide kwa Farao, koma anasonkhetsa dzikoli lipereke ndalamazi; monga mwa lamulo la Farao anasonkhetsa anthu a m'dziko siliva ndi golide, yense monga mwa kuyesedwa kwake, kuzipereka kwa Farao Neko.


Ndipo analamulira mafumu onse kuyambira ku Yufurate kufikira ku dziko la Afilisti, ndi ku malire a ku Ejipito.


Panalinso mafumu amphamvu mu Yerusalemu amene anachita ufumu tsidya lija lonse la mtsinje, ndipo anthu anawapatsa msonkho, thangata, ndi msonkho wa m'njira.


Panali enanso akuti, Takongola ndalama za msonkho wa mfumu; taperekapo chikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa.


Ndipo lichulukitsira mafumu zipatso zake, ndiwo amene munawaika atiweruze, chifukwa cha zoipa zathu; achitanso ufumu pa matupi athu, ndi pa zoweta zathu, monga umo akonda; ndipo ife tisauka kwakukulu.


Kumene akwerako mafuko, ndiwo mafuko a Yehova; akhale mboni ya kwa Israele, Ayamike dzina la Yehova.


Wagwadi kuchokera kumwamba, iwe nthanda, mwana wa mbandakucha! Wagwetsedwa pansi, iwe wolefula amitundu!


Iwe amene wadzala ndi zimfuu, mzinda waphokoso, mzinda wokondwa; ophedwa ako sanaphedwe ndi lupanga, sanafe m'nkhondo.


Ndipo zipata zake zidzalira maliro; ndipo iye adzakhala bwinja, nadzakhala pansi.


Pamenepo udzati m'mtima mwako, Ndani wandibalitsa ine amenewa, popeza ana anga anachotsedwa kwa ine, ndipo ndili wouma, ndi wochotsedwa m'dziko, ndi woyendayenda kwina ndi kwina? Ndipo ndani wadza ndi awa? Taona ndinasiyidwa ndekha, amenewa anali kuti?


Ambuye Yehova watsegula khutu langa, ndipo sindinakhale wopanduka ngakhale kubwerera m'mbuyo.


Dzisanse fumbi; uka, khala tsonga, Yerusalemu; udzimasulire maunyolo a pakhosi pako, iwe mwana wamkazi wam'nsinga wa Ziyoni.


Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu.


Usaope, pakuti sudzakhala ndi manyazi; usasokonezedwe, pakuti sudzachitidwa manyazi; pakuti udzaiwala manyazi a ubwana wako, ndi chitonzo cha umasiye wako sudzachikumbukiranso.


Pakuti Yehova atero, Imbirani Yakobo ndi kukondwa, fuulirani mtundu woposawo; lalikirani, yamikirani, ndi kuti, Yehova, mupulumutse anthu anu, ndi otsala a Israele.


Ndipo Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani anawalumbirira iwo ndi anthu ao, kuti, Musaope kuwatumikira Ababiloni; khalani m'dzikomu, mutumikire mfumu ya ku Babiloni, ndipo kudzakukomerani.


nati kwa Yeremiya mneneri, Chipembedzero chathu chigwe pamaso panu, nimutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha otsala onsewa; pakuti tatsala ife owerengeka m'malo mwa ambiri, monga maso anu ationa ife;


Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Mwaona choipa chonse chimene ndatengera pa Yerusalemu, ndi pa mizinda yonse ya Yuda; ndipo, taonani, lero lomwe ili bwinja, palibe munthu wokhalamo;


Chifukwa chake mkwiyo wanga ndi ukali wanga unathiridwa, nuyaka m'mizinda ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu; ndipo yapasudwa nikhala bwinja, monga lero lomwe.


Nyundo ya dziko lonse yaduka ndi kuthyoka! Babiloni wasanduka bwinja pakati pa amitundu!


Ndipo ndidzayesa Yerusalemu miyulu, mbuto ya ankhandwe; ndipo ndidzayesa mizinda ya Yuda bwinja, lopanda wokhalamo.


Ndinaitana akundikondawo koma anandinyenga; ansembe ndi akulu anga anamwalira m'mzindamu, alikufunafuna zakudya zotsitsimutsa miyoyo yao.


Ambuye waphimbatu ndi mtambo mwana wamkazi wa Ziyoni, pomkwiyira! Wagwetsa pansi kuchokera kumwamba kukoma kwake kwa Israele; osakumbukira poponda mapazi ake tsiku la mkwiyo wake.


Akulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi natonthola; aponya fumbi pa mitu yao, anamangirira chiguduli m'chuuno mwao: Anamwali a ku Yerusalemu aweramitsa pansi mitu yao.


Ha! Golide wagugadi; golide woona woposa wasandulika; miyala ya malo opatulika yakhuthulidwa pa malekezero a makwalala onse.


Korona wagwa pamutu pathu; kalanga ife! Pakuti tinachimwa.


Pamenepo akalonga onse a kunyanja adzatsika ku mipando yachifumu yao, nadzavula zovala zao zopikapika, nadzavala kunjenjemera, nadzakhala panthaka pansi, nadzanjenjemera mphindi zonse ndi kudabwa nawe.


Wobadwa ndi munthu iwe, popeza Tiro ananyodola Yerusalemu, ndi kuti, Ha! Wathyoka uwu udali chipata cha mitundu ya anthu; wanditembenukira ine; ndidzakhuta ine, wapasuka uwu;


Atero Yehova Mulungu, Uwu ndi Yerusalemu ndinauika pakati pa amitundu, ndi pozungulira pake pali maiko.


Ndipo ndidzasandutsa mizinda yanu bwinja, ndi kupasula malo anu opatulika, wosanunkhiza Ine za fungo lanu lokoma.


Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi mizinda yanu idzakhala bwinja.


Uwu ndi mzinda wosekererawo unakhala wosasamalira, unanena m'mtima mwake, Ine ndine, ndi wopanda ine palibe wina; ha! Wasanduka bwinja, mogonera nyama zakuthengo! Yense wakuupitirira adzatsonya mtsonyo, ndi kupukusa mutu.


Monga momwe unadzichitira ulemu, nudyerera, momwemo muuchitire chouzunza ndi chouliritsa maliro: pakuti unena mumtima mwake, Ndikhala ine mfumu, wosati wamasiye ine, wosaona maliro konse ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa