Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 1:19 - Buku Lopatulika

19 Ulemerero wako, Israele, unaphedwa pa misanje yako. Ha! Adagwa amphamvu!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ulemerero wako, Israele, unaphedwa pa misanje yako. Ha! Adagwa amphamvu!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 “Ulemerero wako wathera zitunda zako zachipembedzo, iwe Israele. Ha! Kani amphamvu agwa motere!

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 “Ulemerero wako iwe Israeli, wagona utaphedwa ku zitunda. Taonani amphamvu agwa kumeneko!

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 1:19
11 Mawu Ofanana  

Saulo ndi Yonatani anali okoma ndi okondweretsa m'miyoyo yao, ndipo mu imfa yao sanasiyane; anali nalo liwiro loposa chiombankhanga, anali amphamvu koposa mikango.


Ha! Amphamvuwo anagwa pakati pa nkhondo! Yonatani anaphedwa pamisanje pako.


Ha! Amphamvuwo anagwa, ndi zida za nkhondo zinaonongeka.


Tsiku limenelo mphukira ya Yehova idzakhala yokongola ndi ya ulemerero, chipatso cha nthaka chidzakhala chokometsetsa ndi chokongola, kwa iwo amene adzapulumuka a Israele.


Pakuti ameneyo adzaphuka pamaso pake ngati mtengo wanthete, ndi ngati muzu womera m'nthaka youma; Iye alibe maonekedwe, pena kukongola; ndipo pamene timuona palibe kukongola kuti timkhumbe.


Ambuye waphimbatu ndi mtambo mwana wamkazi wa Ziyoni, pomkwiyira! Wagwetsa pansi kuchokera kumwamba kukoma kwake kwa Israele; osakumbukira poponda mapazi ake tsiku la mkwiyo wake.


Korona wagwa pamutu pathu; kalanga ife! Pakuti tinachimwa.


Ndipo ndinatenga ndodo yanga Chisomo, ndi kuidula pakati, kuti ndiphwanye pangano langa ndinalichita ndi mitundu yonse ya anthu.


M'mwemo ndinadyetsa zoweta zakukaphedwa, ndizo zoweta zonyankhalala. Ndipo ndinadzitengera ndodo ziwiri; ina ndinaitcha Chisomo, inzake ndinaitcha Chomanganitsa; ndipo ndinadyetsa zowetazo.


Ndipo kunali m'mawa mwake, pakubwera Afilisti kuvula akufawo, anapeza Saulo ndi ana ake atatu ali akufa m'phiri la Gilibowa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa