Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 1:20 - Buku Lopatulika

20 Usachinene ku Gati, usachibukitse m'makwalala a Asikeloni, kuti ana aakazi a Afilisti angasekere, kuti ana aakazi a osadulidwawo angafuule mokondwera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Usachinene ku Gati, usachibukitse m'makwalala a Asikeloni, kuti ana akazi a Afilisti angasekere, kuti ana akazi a osadulidwawo angafuule mokondwera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Musakanene zimenezi ku Gati, musakalengeze m'miseu ya ku Asikeloni, kuti akazi a Afilisti angasekerere, akazi a anthu osaumbalidwa angakondwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 “Musakanene zimenezi ku Gati, musazilengeze ku misewu ya ku Asikeloni, kuti ana aakazi a Afilisti angasangalale, ana aakazi a osachita mdulidwe angakondwere.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 1:20
15 Mawu Ofanana  

Taona tsono, ndakutambasulira dzanja langa, ndi kuchepsa gawo lako la chakudya, ndi kukupereka ku chifuniro cha iwo akudana nawe, kwa ana aakazi a Afilisti akuchita manyazi ndi njira yako yoipa.


chisanavundukuke choipa chako monga nthawi ya chitonzo cha ana aakazi a Aramu, ndi onse akumzungulira iye, ana aakazi a Afilisti akupeputsa pozungulira ponse.


Musachifotokoza mu Gati, musalira misozi konse; m'nyumba ya Afira ndinagubuduka m'fumbi.


Pofika Yefita ku Mizipa kunyumba yake, taonani, mwana wake wamkazi anatuluka kudzakomana naye ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe; ndipo iyeyu anali mwana wake mmodzi yekha, analibe mwana wina wamwamuna kapena wamkazi.


Ndipo mzimu wa Yehova unamgwera Samisoni, natsikira iye kwa Asikeloni, nawakantha amuna makumi atatu, natenga zovala zao, nawapatsa omasulira mwambiwo zovala zosinthanitsa. Koma adapsa mtima, nakwera kunka kunyumba ya atate wake.


Ndipo Yonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira ntchito; pakuti palibe chomletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka.


Ndipo Davide analankhula ndi anthu akuima pafupi ndi iye, nati, Adzamchitira chiyani munthu wakupha Mfilisti uyu, ndi kuchotsa tonzo lake pakati pa Israele? Pakuti Mfilisti uyu wosadulidwa ndiye yani, kuti azinyoza makamu a Mulungu wamoyo?


Ine kapolo wanu ndinapha mkango ndi chimbalangondo zonse ziwiri; ndipo Mfilisti uyu wosadulidwa adzakhala ngati mmodzi wa izo, popeza wanyoza makamu a Mulungu wamoyo.


Ndipo kunali pakudza iwo, pamene Davide anabwera atapha Afilistiwo, anthu aakazi anatuluka m'mizinda yonse ya Israele, ndi kuimba ndi kuvina, kuti akakomane ndi mfumu Saulo, ndi malingaka, ndi chimwemwe, ndi zoimbira.


Tsono Saulo ananena ndi wonyamula zida zake, Solola lupanga lako, undipyoze nalo; kuti osadulidwa awa angabwere ndi kundipyoza, ndi kundiseka. Koma wonyamula zida zake anakana; chifukwa anaopa ndithu. Chifukwa chake Saulo anatenga lupanga lake naligwera.


Ndipo amenewa ndiwo mafundo agolide amene Afilisti anabwezera kwa Yehova akhale nsembe yopalamula, kwa Asidodi limodzi, kwa Gaza limodzi, kwa Asikeloni limodzi, kwa Gati limodzi, kwa Ekeroni limodzi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa