Zefaniya 2:15 - Buku Lopatulika15 Uwu ndi mzinda wosekererawo unakhala wosasamalira, unanena m'mtima mwake, Ine ndine, ndi wopanda ine palibe wina; ha! Wasanduka bwinja, mogonera nyama zakuthengo! Yense wakuupitirira adzatsonya mtsonyo, ndi kupukusa mutu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Uwu ndi mudzi wosekererawo unakhala wosasamalira, unanena m'mtima mwake, Ine ndine, ndi wopanda ine palibe wina; ha! Wasanduka bwinja, mogonera nyama za kuthengo! Yense wakuupitirira adzatsonya mtsonyo, ndi kupukusa mutu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Umenewo ndiwo mzinda umene unkadzimva kuti ndi wokhazikika, umene mumtima mwake unkati, “Ine pano! Palibenso wina ai!” Tauwonani m'mene wasakazikira tsopano! Wasanduka bwinja lokhalamo nyama zakuthengo. Aliyense wodutsamo azidzangotsonya nkumapukusa mutu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Umenewu ndiye mzinda wosasamala umene kale unali wotetezedwa. Unkanena kuti mu mtima mwake, “Ine ndine, ndipo palibenso wina wondiposa.” Taonani lero wasanduka bwinja, kokhala nyama zakutchire! Onse owudutsa akuwunyoza ndi kupukusa mitu yawo. Onani mutuwo |