Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Obadiya 1:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 “Anthu akuba akanabwera kwa iwe, kapena anthu olanda zinthu akanafika usiku, aa, tsoka lanji limene likukudikira iwe! Kodi akanangotengako zimene akuzifuna zokha? Ngati anthu othyola mphesa akanafika, kodi akanakusiyiraniko mphesa pangʼono pokha?

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

5 Akakudzera akuba, kapena mbala usiku, (Ha! Waonongeka) sadzaba mpaka adzakhuta kodi? Akakudzera akutchera mphesa sadzasiya khunkha kodi?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Akakudzera akuba, kapena mbala usiku, (Ha! Waonongeka) sadzaba mpaka adzakhuta kodi? Akakudzera akutchera mphesa sadzasiya khunkha kodi?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 “Akuba akabwera usiku, amangotengako zimene akufuna. Okolola akamathyola zipatso, amasiyako zina. Koma inuyo adani anu akupululani kotheratu.

Onani mutuwo Koperani




Obadiya 1:5
13 Mawu Ofanana  

“Ulemerero wako iwe Israeli, wagona utaphedwa ku zitunda. Taonani amphamvu agwa kumeneko!


Wagwa pansi bwanji kuchoka kumwamba, iwe nthanda, mwana wa mʼbandakucha! Wagwetsedwa pansi pa dziko lapansi, Iwe amene unagonjetsapo mitundu ya anthu!


Komabe Aisraeli ochepa okha ndiwo ati adzatsale monga mʼmene zimatsalira zipatso ziwiri kapena zitatu pa nthambi ya pamwamba penipeni kapena zipatso zisanu pa nthambi za mʼmunsi mwa mtengo wa olivi akawugwedeza,” akutero Yehova, Mulungu wa Israeli.


Zimenezi ndizo zidzachitikire mitundu yonse ya dziko lapansi ndiponso pakati pa mitundu ya anthu. Zidzakhala ngati pamene mitengo ya olivi yayoyoledwa, kapena ngati nthawi ya kunkha la mphesa atatsiriza kukolola.


Kodi anthu othyola mphesa akanafika kwa inu akanakusiyiraniko mphesa pangʼono pokha? Anthu akuba akanafika usiku akanangotengako zimene akuzifuna zokha?


Taonani mʼmene waphwanyikira ndi kuwonongekera uja amati ndi nyundo ya dziko lonse lapansi. Mzinda wa Babuloni wasanduka chinthu chochititsa mantha pakati pa mitundu ina!


Yehova Wamphamvuzonse anandiwuza kuti, “Adani adzawakunkha ndithu anthu otsala a Israeli, monga momwe amachitira populula mphesa. Tsono iwe yesetsa kupulumutsa amene ungathe monga mmene amachitira munthu wokolola mphesa.”


Haa! Mzinda uja wasiyidwa wokhawokha, umene kale unali wodzaza ndi anthu! Kale unali wotchuka pakati pa mitundu ya anthu! Tsopano wasanduka ngati mkazi wamasiye. Kale unali mfumukazi ya onse pa dziko lapansi, tsopano wasanduka kapolo.


Ankhondo ako, iwe Temani, adzachita mantha, ndipo aliyense amene ali mʼphiri la Esau adzaphedwa pa nkhondo.


Tsoka ine! Ndili ngati munthu wokunkha zipatso nthawi yachilimwe, pa nthawi yokolola mphesa; palibe phava lamphesa loti nʼkudya, palibe nkhuyu zoyambirira zimene ndimazilakalaka kwambiri.


Umenewu ndiye mzinda wosasamala umene kale unali wotetezedwa. Unkanena kuti mu mtima mwake, “Ine ndine, ndipo palibenso wina wondiposa.” Taonani lero wasanduka bwinja, kokhala nyama zakutchire! Onse owudutsa akuwunyoza ndi kupukusa mitu yawo.


Mukakolola mphesa mʼmunda mwanu musamabwereremonso kachiwiri. Zotsalazo muzilekere alendo, ana ndi akazi amasiye.


Iwo adzayima kutali nalira chifukwa choopsedwa ndi mazunzo ake. “ ‘Tsoka! Tsoka mzinda waukulu iwe, Babuloni mzinda wamphamvu! Mu ora limodzi chiwonongeko chako chafika!’


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa