ndipo Esau anati kwa Yakobo, Undipatse ndidye chofiiracho; chifukwa ndalefuka: chifukwa chake anamutcha dzina lake Edomu.
Obadiya 1:1 - Buku Lopatulika Masomphenya a Obadiya. Atero Ambuye Yehova za Edomu: Tamva mbiri yochokera kwa Yehova, ndi mthenga wotumidwa mwa amitundu, ndi kuti, Nyamukani, timuukire kumthira nkhondo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Masomphenya a Obadiya. Atero Ambuye Yehova za Edomu: Tamva mbiri yochokera kwa Yehova, ndi mthenga wotumidwa mwa amitundu, ndi kuti, Nyamukani, timuukire kumthira nkhondo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Izi ndi zimene Obadiya adaona m'masomphenya. Naŵa mau a Ambuye Chauta onena za Aedomu. Chauta adatuma wamthenga wake kwa anthu a mitundu yonse, ndipo tidamva mau ake, adati, “Konzekani, tiyeni tikamenyane nkhondo ndi Aedomu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Masomphenya a Obadiya. Ambuye Yehova akunena kwa Edomu kuti, Tamva uthenga wochokera kwa Yehova: Nthumwi yatumidwa kupita kwa anthu a mitundu kukanena kuti, “Konzekani, tiyeni tikachite nkhondo ndi Edomu.” |
ndipo Esau anati kwa Yakobo, Undipatse ndidye chofiiracho; chifukwa ndalefuka: chifukwa chake anamutcha dzina lake Edomu.
Yehova, kumbukirani ana a Edomu tsiku la Yerusalemu; amene adati, Gamulani, gamulani, kufikira maziko ake.
Katundu wa Duma. Wina aitana kwa ine kuchokera ku Seiri, Mlonda, nthawi yanji ya usiku? Mlonda, nthawi yanji ya usiku?
Mlonda anati, Kuli kucha, koma kukali usiku; mukafuna kufunsa, funsani, bwerani, idzani.
Ndipo ndinatenga chikho padzanja la Yehova, ndinamwetsa mitundu yonse, imene Yehova ananditumizirako;
Mtima wanu usalefuke, musaope chifukwa cha mbiri imene idzamveka m'dzikomu; pakuti mbiri idzafika chaka china, pambuyo pake chaka china mbiri ina, ndi chiwawa m'dziko, wolamulira kumenyana ndi wolamulira.
Ejipito adzasanduka bwinja, ndi Edomu adzasanduka chipululu chopanda kanthu, chifukwa cha chiwawachi anawachitira ana a Yuda; popeza anakhetsa mwazi wosachimwa m'dziko lao.
Wothyola wakwera pamaso pao; iwo anathyola, napita kuchipata, natuluka pomwepo; ndi mfumu yao yapita pamaso pao, ndipo Yehova awatsogolera.
Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma chitsiriziro sichinafike.
Ndipo m'mene mudzamva za nkhondo ndi mbiri zake za nkhondo, musamadera nkhawa: ziyenera kuchitika izi; koma sichinafike chimaliziro.