Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 25:30 - Buku Lopatulika

30 ndipo Esau anati kwa Yakobo, Undipatse ndidye chofiiracho; chifukwa ndalefuka: chifukwa chake anamutcha dzina lake Edomu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 ndipo Esau anati kwa Yakobo, Undipatse ndidye chofiiracho; chifukwa ndalefuka: chifukwa chake anamutcha dzina lake Edomu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Anali ndi njala zedi, motero adauza Yakobe kuti, “Ine njala yandipha. Patseko nyemba zofiira waphikazi.” (Nchifukwa chake adamutcha Edomu.)

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Iye anati kwa Yakobo, “Tandipatsako phala lofiiralo, ndimwe! Ndalefuka ndi njala.” (Nʼchifukwa chake amatchedwanso Edomu).

Onani mutuwo Koperani




Genesis 25:30
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anaphika mphodza: ndipo Esau anachokera kuthengo, nalefuka:


Ndipo Yakobo anati, Tigulane lero ukulu wako.


Ndipo Yakobo anatumiza amithenga patsogolo pake kwa Esau mkulu wake, ku dziko la Seiri, kudera la ku Edomu.


Ndipo anauza iwo kuti, Mukanene chotere kwa mbuyanga Esau: Atero Yakobo kapolo wako, ndakhala pamodzi naye Labani, ndipo ndakhalabe kufikira tsopano lino:


Mibadwo ya Esau (ndiye Edomu) ndi iyi:


Amenewa ndi ana aamuna a Esau, amenewa ndi mafumu ao; yemweyo ndi Edomu.


mfumu Magadiele, mfumu Iramu; amenewa ndi mafumu a Edomu, monga mwa kukhala kwao m'dziko lokhala laolao. Uyo ndiye Esau atate wao wa Aedomu.


Ndipo Esau anakhala m'phiri la Seiri; Esau ndiye Edomu.


Mibadwo ya Esau atate wao wa Aedomu m'phiri la Seiri ndi iyi:


Masiku ake Aedomu anapanduka ku ulamuliro wa Yuda, nadziikira mfumu okha.


Pamenepo mafumu a Edomu anadabwa; agwidwa nako kunthunthumira amphamvu a ku Mowabu; okhala mu Kanani onse asungunuka mtima.


Za Edomu. Yehova wa makamu atero: Kodi mu Temani mulibenso nzeru? Kodi uphungu wawathera akuchenjera? Kodi nseru zao zatha psiti?


Masomphenya a Obadiya. Atero Ambuye Yehova za Edomu: Tamva mbiri yochokera kwa Yehova, ndi mthenga wotumidwa mwa amitundu, ndi kuti, Nyamukani, timuukire kumthira nkhondo.


Musamanyansidwa naye Mwedomu, popeza ndiye mbale wanu; musamanyansidwa naye Mwejipito, popeza munali alendo m'dziko lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa