Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 13:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo m'mene mudzamva za nkhondo ndi mbiri zake za nkhondo, musamadera nkhawa: ziyenera kuchitika izi; koma sichinafike chimaliziro.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo m'mene mudzamva za nkhondo ndi mbiri zake za nkhondo, musamadera nkhawa: ziyenera kuchitika izi; koma sichinafike chimaliziro.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Koma inu mukadzamva phokoso la nkhondo za kufupi kuno, kapena mphekesera za nkhondo zakutali, musadzade nkhaŵa ai. Zimenezi zidzayenera kuchitika, koma sindiye kuti chimalizo chija chafika kale ai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Pamene mudzamva zankhondo ndi mbiri zankhondo, musadzadzidzimuke. Zinthu zotere ziyenera kuchitika, koma sikuti chimaliziro chafika kale ayi.

Onani mutuwo Koperani




Marko 13:7
17 Mawu Ofanana  

Pakuti kufa tidzafa, ndipo tili ngati madzi otayika pansi amene sangathe kuwaolanso; ngakhale Mulungu sachotsa moyo, koma alingalira njira yakuti wotayikayo asakhale womtayikira Iye.


Sadzaopa mbiri yoipa; mtima wake ngwokhazikika, wokhulupirira Yehova.


Lingakhale gulu la ankhondo limanga misasa kuti andithyole, mtima wanga sungachite mantha; ingakhale nkhondo ikandiukira, inde pomweponso ndidzakhulupirira.


Usaope zoopsa zodzidzimutsa, ngakhale zikadza zopasula oipa;


Musachinene, Chiwembu; chilichonse chimene anthu awa adzachinena, Chiwembu; musaope monga kuopa kwao kapena musachite mantha.


Mtima wanu usalefuke, musaope chifukwa cha mbiri imene idzamveka m'dzikomu; pakuti mbiri idzafika chaka china, pambuyo pake chaka china mbiri ina, ndi chiwawa m'dziko, wolamulira kumenyana ndi wolamulira.


Tsoka lili ndi dziko lapansi chifukwa cha zokhumudwitsa! Pakuti sikutheka kuti zokhumudwitsa zileke kudza, koma tsoka lili ndi munthu amene chokhumudwitsacho chidza ndi iye.


Ndipo Herode mfumuyo pakumva ichi anavutika, ndi Yerusalemu yense pamodzi naye.


Ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Iye; nadzasocheretsa ambiri.


Pakuti mtundu wa anthu udzayambana ndi mtundu wina, ndipo ufumu ndi ufumu unzake: padzakhala zivomezi m'malo m'malo; padzakhala njala; izi ndi zoyambira za zowawa.


Mtima wanu usavutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso.


Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.


natsimikiza, kuti kunayenera Khristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Khristu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa