Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Obadiya 1:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Masomphenya a Obadiya. Ambuye Yehova akunena kwa Edomu kuti, Tamva uthenga wochokera kwa Yehova: Nthumwi yatumidwa kupita kwa anthu a mitundu kukanena kuti, “Konzekani, tiyeni tikachite nkhondo ndi Edomu.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Masomphenya a Obadiya. Atero Ambuye Yehova za Edomu: Tamva mbiri yochokera kwa Yehova, ndi mthenga wotumidwa mwa amitundu, ndi kuti, Nyamukani, timuukire kumthira nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Masomphenya a Obadiya. Atero Ambuye Yehova za Edomu: Tamva mbiri yochokera kwa Yehova, ndi mthenga wotumidwa mwa amitundu, ndi kuti, Nyamukani, timuukire kumthira nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Izi ndi zimene Obadiya adaona m'masomphenya. Naŵa mau a Ambuye Chauta onena za Aedomu. Chauta adatuma wamthenga wake kwa anthu a mitundu yonse, ndipo tidamva mau ake, adati, “Konzekani, tiyeni tikamenyane nkhondo ndi Aedomu.”

Onani mutuwo Koperani




Obadiya 1:1
28 Mawu Ofanana  

Iye anati kwa Yakobo, “Tandipatsako phala lofiiralo, ndimwe! Ndalefuka ndi njala.” (Nʼchifukwa chake amatchedwanso Edomu).


Choncho Esau (amene ndi Edomu) anakakhazikika ku dziko la mapiri ku Seiri.


Nazi zidzukulu za Esau, kholo la Aedomu amene ankakhala ku Seiri.


Kumbukirani, Inu Yehova, zimene Aedomu anachita pa tsiku limene Yerusalemu anagonja. Iwowo anafuwula kuti, “Mugwetseni pansi, mugwetseni pansi mpaka pa maziko ake!”


Uthenga wonena za Duma: Munthu wina akundiyitana kuchokera ku Seiri kuti, “Iwe mlonda, usikuwu utha liti? Iwe mlonda, utha liti kodi usikuwu?”


Mlonda akuyankha kuti, “Kukucha, koma kudanso. Ngati ukufuna kufunsa, funsa tsopano; ndipo ubwerenso udzafunse.”


Ngakhale kuti nduna zawo zili ku Zowani, ndipo akazembe awo afika kale ku Hanesi,


Choncho ine ndinatenga chikhocho mʼdzanja la Yehova ndipo ndinamwetsa mitundu yonse ya anthu kumene Iye ananditumako:


Edomu, Mowabu ndi Amoni.


Musataye mtima kapena kuchita mantha pamene mphekesera zikumveka mʼdziko mwanu. Chaka ndi chaka pamabuka mphekesera za ziwawa mʼdziko lapansi, ndiponso yakuti mfumu yakuti ikuthira nkhondo mfumu ina.


Yehova anandiyankhula kuti:


Koma Igupto adzasanduka bwinja, Edomu adzasanduka chipululu, chifukwa cha nkhondo imene anathira anthu a ku Yuda mʼdziko limene anakhetsa magazi a anthu osalakwa.


Amene adzawapulumutse adzayenda patsogolo pawo; iwo adzathyola chipata ndipo adzatuluka. Mfumu yawo idzawatsogolera, Yehova adzakhala patsogolo pawo.”


Mudzamva za nkhondo ndi mbiri za nkhondo, koma onetsetsani kuti musadzidzimuke nazo. Zotere ziyenera kuchitika, koma chimaliziro sichinafike.


Pamene mudzamva zankhondo ndi mbiri zankhondo, musadzadzidzimuke. Zinthu zotere ziyenera kuchitika, koma sikuti chimaliziro chafika kale ayi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa