Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -

Masalimo 137 - Buku Lopatulika


Kudandaula kwa Ayuda ku Babiloni

1 Ku mitsinje ya ku Babiloni, kumeneko tinakhala pansi, inde tinalira, pokumbukira Ziyoni.

2 Pa msondodzi uli m'mwemo tinapachika mazeze athu.

3 Popeza pamenepo akutigwirawo anatifunsa nyimbo ndipo akutizunza anafuna tisekere, ndi kuti, Mutiimbire nyimbo imodzi ya ku Ziyoni.

4 Tidati, Tidzaimba bwanji nyimbo ya Yehova m'dziko lachilendo?

5 Ndikakuiwalani, Yerusalemu, dzanja lamanja langa liiwale luso lake.

6 Lilime langa limamatike kunsaya zanga, ndikapanda kukumbukira inu; ndikapanda kusankha Yerusalemu koposa chimwemwe changa chopambana.

7 Yehova, kumbukirani ana a Edomu tsiku la Yerusalemu; amene adati, Gamulani, gamulani, kufikira maziko ake.

8 Mwana wamkazi wa ku Babiloni, iwe amene udzapasulidwa; wodala iye amene adzakubwezera chilango monga umo unatichitira ife.

9 Wodala iye amene adzagwira makanda ako, ndi kuwaphwanya pathanthwe.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi
Titsatireni:



Zotsatsa