ndipo uitchinge pa mizati inai ya mitengo wakasiya, zokuta ndi golide; zokowera zao zikhale zagolide, ndi makamwa anai asiliva.
Numeri 3:36 - Buku Lopatulika Ndipo choyang'anira iwo, udikiro wao wa ana a Merari ndiwo matabwa a chihema, ndi mitanda yake, ndi mizati ndi nsanamira zake, ndi makamwa ake, ndi zipangizo zake zonse, ndi ntchito zake zonse; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo choyang'anira iwo, udikiro wao wa ana a Merari ndiwo matabwa a Kachisi, ndi mitanda yake, ndi mizati ndi nsanamira zake, ndi makamwa ake, ndi zipangizo zake zonse, ndi ntchito zake zonse; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ntchito imene ana aamuna a Merari adapatsidwa, inali yosamala mitengo ya malo opatulika monga: nsichi zake, mizati yake, masinde ake ndi zina zonse zoyendera limodzi ndi zimenezo. Ankayang'anira ntchito zonse zokhudza zimenezi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amerari anapatsidwa ntchito yosamalira mitengo ya chihema, nsichi zake, mizati yake, matsinde ake, ndi zida zake zonse, ndi zonse zomwe ankagwiritsa ntchito, |
ndipo uitchinge pa mizati inai ya mitengo wakasiya, zokuta ndi golide; zokowera zao zikhale zagolide, ndi makamwa anai asiliva.
Ndipo uzipangira nsalu yotsekerayo nsanamira zisanu za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide; zokowera zao zikhale zagolide; nuziyengera makamwa asanu amkuwa.
chihema, ndi chophimba chake, zokowera zake, ndi matabwa ake, mitanda yake, mizati, nsanamira, ndi nsichi zake, ndi makamwa ao;
Ndipo anaipangira mizati inai ya kasiya, nazikuta ndi golide; zokowera zao zinali zagolide; ndipo anaziyengera makamwa anai asiliva.
Ndipo anabwera naye Kachisi kwa Mose, chihemacho, ndi zipangizo zake zonse, zokowera zake, matabwa ake, mitanda yake, ndi mizati yake, nsanamira zake ndi nsichi zake, ndi makamwa ake;
Ndi kalonga wa nyumba ya makolo ya mabanja la Merari ndiye Zuriyele mwana wa Abihaili; azimanga mahema ao pa mbali ya chihema cha kumpoto.
napatsa ana a Merari magaleta anai ndi ng'ombe zisanu ndi zitatu, monga mwa ntchito yao; wakuziyang'anira ndiye Itamara mwana wa Aroni wansembe.