Eksodo 26:32 - Buku Lopatulika32 ndipo uitchinge pa mizati inai ya mitengo wakasiya, zokuta ndi golide; zokowera zao zikhale zagolide, ndi makamwa anai asiliva. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201432 ndipo uichinge pa mizati inai ya mitengo wakasiya, zokuta ndi golide; zokowera zao zikhale zagolide, ndi makamwa anai asiliva. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa32 Uikoloŵeke pa nsanamira zinai zakasiya zokutidwa ndi golide, zokhala ndi ngoŵe zagolide ndi zokhazikika pa masinde anai asiliva. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero32 Nsaluyo uyikoloweke pa nsanamira zinayi zamtengo wa mkesha zokutidwa ndi golide zomwe zili ndi ngowe zagolide, zomwe zayima pa matsinde asiliva anayi. Onani mutuwo |