Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 26:37 - Buku Lopatulika

37 Ndipo uzipangira nsalu yotsekerayo nsanamira zisanu za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide; zokowera zao zikhale zagolide; nuziyengera makamwa asanu amkuwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

37 Ndipo uzipangira nsalu yotsekerayo nsanamira zisanu za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide; zokowera zao zikhale zagolide; nuziyengera makamwa asanu amkuwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

37 Upange nsanamira zisanu zakasiya zimene akoloŵekepo nsalu yochingayo. Zikutidwe ndi golide, ndipo ngoŵe zake zokoloŵekapo zikhalenso zagolide, ndiponso upange masinde asanu amkuŵa a nsanamira zimenezo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

37 Upange ngowe zagolide za nsaluyo ndi nsanamira zisanu zamtengo wa mkesha ndipo uzikute ndi golide. Upangenso matsinde asanu amkuwa a nsanamirazo.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 26:37
4 Mawu Ofanana  

Ndipo ulikute ndi golide woona, ulikute m'kati ndi kubwalo, nulipangire mkombero wagolide pozungulira pake.


ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wakasiya;


ndi nsanamira zake zisanu ndi zokowera zao; nakuta mitu yao ndi mitanda yao ndi golide; ndi makamwa ao asanu anali amkuwa.


Ndipo anapanga nao makamwa a pa khomo la chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe lamkuwa, ndi sefa wake amkuwa, ndi zipangizo zonse za guwa la nsembe,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa