Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 27:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo upange guwa la nsembe la mtengo wakasiya, utali wake mikono isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu, guwa la nsembelo likhale laphwamphwa, ndi msinkhu wake mikono itatu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo upange guwa la nsembe la mtengo wakasiya, utali wake mikono isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu, guwa la nsembelo likhale laphwamphwa, ndi msinkhu wake mikono itatu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 “Upange guwa la nsembe zopsereza la matabwa a mtengo wa kasiya. Likhale lalibanda: muutali mwake likhale masentimita 229, muufupi mwake chimodzimodzi: masentimita 229, msinkhu wake masentimita 137.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 “Upange guwa lansembe lamatabwa amtengo wa mkesha. Likhale lofanana mbali zonse, msinkhu wake masentimita 137, mulitali mwake masentimita 229, mulifupi mwake masentimita 229.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 27:1
20 Mawu Ofanana  

Ndipo Gadi anafika tsiku lomwelo kwa Davide nanena naye, Kwerani mukamangire Yehova guwa la nsembe pa dwale la Arauna Myebusi.


Nalichotsa guwa la nsembe lamkuwa linali pamaso pa Yehova, nalichotsa ku khomo la nyumba pakati paguwa lake la nsembe ndi nyumba ya Yehova, naliika kumpoto kwa guwa lake la nsembe.


Koma Aroni ndi ana ake ankafukiza paguwa la nsembe yopsereza, ndi paguwa la nsembe yofukiza, chifukwa cha ntchito yonse ya malo opatulika kwambiri, ndi kuchitira Israele chowatetezera, monga mwa zonse Mose mtumiki wa Mulungu adawauza.


Anapanganso guwa la nsembe lamkuwa, m'litali mwake mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono khumi.


Nanyamuka Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ake ansembe, ndi Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi abale ake, namanga guwa la nsembe la Mulungu wa Israele, kuperekapo nsembe zopsereza, monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose munthu wa Mulungu.


Ndipo Mose anamanga guwa la nsembe, nalitcha dzina lake Yehova Nisi:


Ndipo Mose analembera mau onse a Yehova, nalawira kuuka mamawa, namanga guwa la nsembe patsinde paphiri, ndi zoimiritsa khumi ndi ziwiri, kwa mafuko khumi ndi awiri a Israele.


ndi guwa la nsembe yopsereza ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate ndi tsinde lake;


guwa la nsembe yopsereza, ndi sefa wamkuwa, mphiko zake, ndi zipangizo zake zonse, mkhate ndi tsinde lake;


guwa la nsembe la mkuwa, ndi sefa wake wamkuwa, mphiko zake, ndi zipangizo zake zonse, mkhate ndi tsinde lake;


Ndipo udzoze guwa la nsembe yopsereza, ndi zipangizo zake zonse, ndi kulipatula guwalo; ndipo guwalo lidzakhala lopatulika kwambiri.


Ndipo anaika guwa la nsembe yopsereza pa khomo la Kachisi wa chihema chokomanako, natenthapo nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa; monga Yehova adamuuza Mose.


Ndipo ukaike guwa la nsembe yopsereza kunja kwa khomo la Kachisi wa chihema chokomanako.


Ndipo udikiro wao ndiwo likasa, ndi gome, ndi choikaponyali, ndi maguwa a nsembe, ndi zipangizo za malo opatulika zimene achita nazo, ndi nsalu yotchinga, ndi ntchito zake zonse.


Ndipo azichotsa mapulusa paguwa la nsembe, ndi kuyala pa ilo nsalu yofiirira.


Naikepo zipangizo zake zonse, zimene atumikira nazo pamenepo, mbale za zofukiza, mitungo, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, zipangizo zonse za guwa la nsembe; nayalepo chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake.


Tili nalo guwa la nsembe, limene iwo akutumikira chihema alibe ulamuliro wa kudyako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa