Numeri 22:32 - Buku Lopatulika Ndipo mthenga wa Yehova ananena naye, Wapandiranji bulu wako katatu tsopano? Taona, ndatuluka kuti nditsutsane nawe popeza njira iyi ikugwetsa chamutu pamaso panga; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mthenga wa Yehova ananena naye, Wapandiranji bulu wako katatu tsopano? Taona, ndatuluka kuti nditsutsane nawe popeza njira iyi ikugwetsa chamtu pamaso panga; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mngelo wa Chauta adamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani wamenya bulu wako chotere katatu? Ndabwera kudzakutsekera njira, chifukwa ulendo wakowu ukundiipira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mngelo wa Yehova anamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani wamenya bulu wako katatu? Taona, Ine ndabwera kudzakutsutsa chifukwa ulendo wakowu ndi woyipa pamaso panga. |
Chilungamo chanu chikunga mapiri a Mulungu; maweruzo anu akunga chozama chachikulu, Yehova, musunga munthu ndi nyama.
Waumphawi woyenda mwangwiro apambana ndi yemwe akhotetsa njira zake, angakhale alemera.
ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Ninive mzinda waukulu uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati padzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?
Anthu anga, kumbukiranitu chofunsira Balaki mfumu ya Mowabu, ndi chomuyankha Balamu mwana wa Beori, kuyambira ku Sitimu kufikira ku Giligala; kuti mudziwe zolungama za Yehova.
Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu usiku, nanena naye, Akadza kukuitana anthuwa, nyamuka, kunka nao, koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukachite.
Koma anapsa mtima Mulungu chifukwa cha kupita iye, ndipo mthenga wa Yehova anadziika m'njira wotsutsana naye. Ndipo anali wokwera pabulu wake, ndi anyamata ake awiri anali naye.
Ndipo Yehova anatsegula pakamwa pake pa bulu, nati uyu kwa Balamu, Ndakuchitanji, kuti wandipanda katatu tsopano?
koma bulu anandiona, nandipatukira nthawi izi zitatu pondiona; akadapanda kundipatukira, ndikadakupha iwe ndithu, ndi kumsunga iye wamoyo.
Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Balamu, Pita nao anthuwa; koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukanene. Potero Balamu anamuka nao akalonga a Balaki.
nati, Wodzala ndi chinyengo chonse ndi chenjerero lonse, iwe, mwana wa mdierekezi, mdani wa chilungamo chonse, kodi sudzaleka kuipsa njira zolunjika za Ambuye?
popeza sanakumane nanu ndi mkate ndi madzi m'njira muja munatuluka mu Ejipito; popezanso anakulembererani Balamu mwana wa Beori wa ku Petori wa Mesopotamiya, kuti akutemberereni.