Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 22:22 - Buku Lopatulika

22 Koma anapsa mtima Mulungu chifukwa cha kupita iye, ndipo mthenga wa Yehova anadziika m'njira wotsutsana naye. Ndipo anali wokwera pabulu wake, ndi anyamata ake awiri anali naye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Koma anapsa mtima Mulungu chifukwa cha kupita iye, ndipo mthenga wa Yehova anadziika m'njira wotsutsana naye. Ndipo anali wokwera pa bulu wake, ndi anyamata ake awiri anali naye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Komabe Mulungu adapsa mtima chifukwa choti Balamuyo adapita. Ndipo mngelo wa Chauta adaimirira mu mseu, kuti amtsekere njira. Pamenepo nkuti atakwera bulu, ndipo ali ndi anyamata ake aŵiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Koma Mulungu anakwiya kwambiri pamene ankapita ndipo mngelo wa Yehova anayima pa njira kutsutsana naye. Balaamu anakwera bulu wake wamkazi ndipo antchito ake awiri anali naye.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 22:22
11 Mawu Ofanana  

Nati Yehu, Lalikirani msonkhano wopatulika wa Baala. Naulalikira.


Taona, ndituma mthenga akutsogolere, kukusunga panjira, ndi kukufikitsa pamaso pomwe ndakonzeratu.


Ndipo kunali panjira, kuchigono, Yehova anakomana naye, nafuna kumupha.


Wathifula uta wake ngati mdani, waima ndi dzanja lake lamanja ngati mmaliwongo; wapha onse okondweretsa maso; watsanulira ukali wake ngati moto pahema wa mwana wamkazi wa Ziyoni.


Ndipo Yehova anati kwa iye, Umutche dzina lake Yezireele; pakuti katsala kanthawi, ndipo ndidzabwezera chilango mwazi wa Yezireele pa nyumba ya Yehu, ndi kuleketsa ufumu wa nyumba ya Israele.


Ndipo buluyo anaona mthenga wa Yehova alikuima m'njira, ndi lupanga lake ku dzanja lake; ndi bulu anapatuka m'njira, nalowa kuthengo; ndipo Balamu anampanda bulu kumbwezera kunjira.


Ndipo mthenga wa Yehova ananena naye, Wapandiranji bulu wako katatu tsopano? Taona, ndatuluka kuti nditsutsane nawe popeza njira iyi ikugwetsa chamutu pamaso panga;


Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Balamu, Pita nao anthuwa; koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukanene. Potero Balamu anamuka nao akalonga a Balaki.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa