Numeri 19:22 - Buku Lopatulika Ndipo chilichonse munthu wodetsedwa achikhudza chidzakhala chodetsedwa; ndi munthu wakuchikhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo chilichonse munthu wodetsedwa achikhudza chidzakhala chodetsedwa; ndi munthu wakuchikhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chinthu chilichonse chimene munthu woipitsidwa akhudza, chidzakhala choipitsidwa. Ndipo munthu aliyense wokhudza chimenecho, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chilichonse chimene munthu wodetsedwayo achikhudze chidzakhala chodetsedwa ndiponso aliyense wochikhudza adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.” |
Ndipo munthu aliyense akakhudza kanthu kalikonse kadali pansi pake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo iye wakunyamula zimenezo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
Ndipo munthu aliyense wakukhayo akamkhudza, osasambatu m'manja m'madzi, atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
Ndipo aliyense akhudza kama wake azitsuka zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
Ndipo aliyense akhudza chinthu chilichonse akhalapo iye, atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
Ndipo chikakhala pakama, kapena pa chinthu chilichonse akhalapo iye, atachikhudza, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
Ndipo munthu aliyense akakhudza zimenezi adzakhala wodetsedwa, natsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
Ndipo munthu aliyense wakukhudza kama wake azitsuka zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
Ndipo iye wakukhalira chinthu chilichonse adachikhalira wakukhayo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
Ndipo iye wakukhudza thupi la uyo wakukhayo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
Ndipo wakukhayo akalavulira wina woyera; pamenepo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
ndi aliyense wokhudza chinthu chokwawa chakudetsedwa nacho, kapenanso munthu amene akamdetsa nacho, chodetsa chake chilichonse;
munthu wokhudza chilichonse chotere adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo, ndipo asadye zinthu zopatulika, akapanda kusamba thupi lake ndi madzi.
kapena munthu akakhudza chilichonse chodetsa kapena mtembo wa nyama yodetsa, kapena mtembo wa choweta chodetsa, kapena mtembo wa chokwawa chodetsa, kungakhale kudambisikira, ali wodetsedwa, ndi wopalamula.
Kapena akakhudza chodetsa cha munthu, ndicho chodetsa chilichonse akhala wodetsedwa nacho, ndipo chidambisikira; koma pochizindikira akhala wopalamula:
Ndipo nyama yokhudza kanthu kalikonse kodetsa isadyeke; aitenthe ndi moto. Koma za nyama ina, aliyense ayera aidyeko.
Ndipo munthu akakhudza chinthu chodetsa, chodetsa cha munthu, kapena chodetsa cha zoweta, kapena chilichonse chonyansa chodetsa, nakadyako nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, munthuyo achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.
Pamenepo Hagai anati, Munthu wodetsedwa ndi mtembo akakhudza kanthu ka izi, kodi kali kodetsedwa kanthuka? Ndipo ansembe anayankha nati, Kadzakhala kodetsedwa.
Pamenepo wansembe atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi; ndipo atatero alowenso kuchigono; koma wansembeyo adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.