Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 19:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo likhale kwa iwo lemba losatha; kuti iye wakuwaza madzi akusiyanitsa azitsuka zovala zake; ndi iye wakukhudza madzi akusiyanitsa adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo likhale kwa iwo lemba losatha; kuti iye wakuwaza madzi akusiyanitsa azitsuka zovala zake; ndi iye wakukhudza madzi akusiyanitsa adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Limeneli likhale lamulo lamuyaya kwa iwo. Munthu amene awaza madzi oyeretserawo, achape zovala zake. Ndipo munthu amene akhudza madzi ochapirawo, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Ili ndi lamulo lokhazikika kwa iwo. “Munthu amene amawaza madzi oyeretsawo ayenera kuchapa zovala zake ndipo yense wokhudza madzi oyeretserawo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 19:21
12 Mawu Ofanana  

Aroni ndi ana ake aikonze m'chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kunja kwa nsalu yotchinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israele.


ndipo aliyense akanyamulako nyama ya mtembo wake azitsuka zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Ndipo iye wakudya kanthu ka mtembo wake azitsuka zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; iyenso wakunyamula mtembo wake atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Koma Alevi azichita ntchito ya chihema chokomanako, iwo ndiwo azisenza mphulupulu yao; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; ndipo asakhale nacho cholowa pakati pa ana a Israele.


Ndipo wakuola mapulusayo a ng'ombe yaikazi atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo likhale lemba losatha kwa ana a Israele, ndi kwa mlendo wakukhala pakati pao.


Pamenepo wansembe atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi; ndipo atatero alowenso kuchigono; koma wansembeyo adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Ndipo iye wakutentha ng'ombeyo atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Pakuti sikutheka kuti mwazi wa ng'ombe zamphongo, ndi mbuzi ukachotsera machimo.


(pakuti chilamulo sichinachitire kanthu kakhale kopanda chilema), ndipo kulinso kulowa nacho chiyembekezo choposa, chimene tiyandikira nacho kwa Mulungu.


Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyanasiyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa