Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 5:2 - Buku Lopatulika

2 kapena munthu akakhudza chilichonse chodetsa kapena mtembo wa nyama yodetsa, kapena mtembo wa choweta chodetsa, kapena mtembo wa chokwawa chodetsa, kungakhale kudambisikira, ali wodetsedwa, ndi wopalamula.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 kapena munthu akakhudza chilichonse chodetsa kapena mtembo wa nyama yodetsa, kapena mtembo wa choweta chodetsa, kapena mtembo wa chokwawa chodetsa, kungakhale kudambisikira, ali wodetsedwa, ndi wopalamula.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Munthu akakhudza chinthu chilichonse chonyansa pa zachipembedzo, monga nyama yakufa yam'thengo kapena yoŵeta, kapenanso zokwaŵa zakufa, ndipo pokhudzapo adziipitsa mosadziŵa, munthu ameneyo ndi woipitsidwa, ndiponso ndi wopalamula.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “ ‘Munthu akakhudza chinthu chilichonse chodetsedwa, monga nyama yakufa ya mʼthengo, kapena chiweto chakufa kapenanso chokwawa chakufa, ngakhale iyeyo wachikhudza mosadziwa, wasanduka wodetsedwa ndipo wachimwa.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 5:2
16 Mawu Ofanana  

Adziwitsa zolowereza zake ndani? Mundimasule kwa zolakwa zobisika.


Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babiloni; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova.


inde muziyese zonyansa; musamadya nyama zao; mitembo yao zikunyansireni.


Nyama yake musamaidya, mitembo yake musamaikhudza; muziyese zodetsedwa.


Ndipo gulu lonse la Israele likalakwa osati dala, ndipo chikabisika chinthuchi pamaso pa msonkhano, litachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, ndi kupalamula;


Ndipo munthu akachimwa, nakachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova; angakhale analibe kudziwa, koma wapalamula, azisenza mphulupulu yake.


Kapena akakhudza chodetsa cha munthu, ndicho chodetsa chilichonse akhala wodetsedwa nacho, ndipo chidambisikira; koma pochizindikira akhala wopalamula:


kapena munthu akalumbira ndi milomo yake osalingirira kuchita choipa, kapena kuchita chabwino, chilichonse munthu akalumbira osalingirira, ndipo chidambisikira; koma pochizindikira akhala wopalamula chimodzi cha izi:


Ndipo munthu akakhudza chinthu chodetsa, chodetsa cha munthu, kapena chodetsa cha zoweta, kapena chilichonse chonyansa chodetsa, nakadyako nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, munthuyo achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.


Pamenepo Hagai anati, Munthu wodetsedwa ndi mtembo akakhudza kanthu ka izi, kodi kali kodetsedwa kanthuka? Ndipo ansembe anayankha nati, Kadzakhala kodetsedwa.


Ndipo chilichonse munthu wodetsedwa achikhudza chidzakhala chodetsedwa; ndi munthu wakuchikhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Tsoka inu! Chifukwa muli ngati manda osaoneka, ndipo anthu akuyendayenda pamwamba pao sadziwa.


Chifukwa chake, Tulukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye, Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu,


ndi nkhumba, popeza igawanika chiboda koma yosabzikula, muiyese yodetsa; musamadya nyama yao, musamakhudza mitembo yao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa