Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 5:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo akachimwa munthu, wakuti adamva mau akuwalumbiritsa, ndiye mboni, kapena wakuona, kapena wakudziwa, koma osawulula, azisenza mphulupulu yake;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo akachimwa munthu, wakuti adamva mau akuwalumbiritsa, ndiye mboni, kapena wakuona, kapena wakudziwa, koma osawulula, azisenza mphulupulu yake;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 “Munthu akaitanidwa ku bwalo la milandu, namlumbiritsa kuti achite umboni wa zinthu zimene adaziwona kapena adazidziŵa, iyeyo nakana kupereka umboniwo, munthu ameneyo ndi woyenera kumlanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 “ ‘Ngati munthu anayitanidwa ku bwalo kuti akachitire umboni pa zimene anaziona kapena kuzimva koma iye nʼkukana kuchitira umboni, munthu ameneyo wachimwa ndipo ayenera kulangidwa.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 5:1
22 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu inati, Ndikulumbiritse kangati kuti undiuze zoona zokhazokha m'dzina la Yehova?


Ngati munthu akachimwira mnzake, ndi lumbiro likaikidwa pa iye kumlumbiritsa, ndipo akadzalumbira patsogolo pa guwa la nsembe lanu m'nyumba ino;


Ndipo mfumu inati naye, Ndikulumbiritse kangati kuti unene nane choonadi chokhachokha m'dzina la Yehova?


Pakuti mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga; ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera.


lumbiro la Yehova likhale pakati pa iwo awiri, kuti sanatulutse dzanja lake pa chuma cha mnansi wake; ndipo mwiniyo azivomereza, ndipo asalipe.


Woyenda ndi mbala ada moyo wakewake; amva kulumbira, koma osawulula kanthu.


ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.


Iye adzaona zotsatira mavuto a moyo wake, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zake mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zao.


Pakuti dziko ladzala ndi achigololo; pakuti chifukwa cha temberero dziko lirira, mabusa a kuchipululu auma; kuyenda kwao kuli koipa, ndi mphamvu yao siili yabwino.


Moyo wochimwawo ndiwo udzafa; mwana sadzasenza mphulupulu za atate wake, ndi atate sadzasenza mphulupulu za mwana; chilungamo cha wolungama chidzamkhalira, ndi choipa cha woipa chidzamkhalira,


Taonani, miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wochimwawo ndiwo udzafa.


Koma akapanda kuzitsuka, kapena kusamba thupi lake, adzasenza mphulupulu yake.


koma aliyense akudyako adzasenza mphulupulu yake, popeza waipsa chopatulidwa cha Yehova; ndi munthuyu amsadze, kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.


Munthu akatenga mlongo wake, mwana wamkazi wa atate wake, kapena mwana wamkazi wa mai wake, nakaona thupi lake, ndi mlongoyo akaona thupi lake; chochititsa manyazi ichi; ndipo awasadze pamaso pa ana a anthu ao; anavula mlongo wake; asenze mphulupulu yake.


Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Munthu akachimwa, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, nakachitapo kanthu;


Munthu akachita mosakhulupirika, nakachimwa osati dala, pa zopatulika za Yehova, azidza nayo nsembe yake yopalamula kwa Yehova, ndiyo nkhosa yamphongo yopanda chilema, ya m'gulu lake, monga umayesa mtengo wake potchula masekeli a siliva, kunena sekeli wa malo opatulika, ikhale nsembe yopalamula;


Ndipo munthu akachimwa, nakachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova; angakhale analibe kudziwa, koma wapalamula, azisenza mphulupulu yake.


Ndipo akadyako nyama ya nsembe zoyamika zake tsiku lachitatu, sikuvomerezeka kumene; sadzamwerengera wobwera nayo; ndiyo chinthu chonyansa, ndipo munthu wakudyako adzasenza mphulupulu zake.


Munthu akakhala woyera, wosakhala paulendo, koma akaleka kuchita Paska, amsadze munthuyo kwa anthu a mtundu wake; popeza sanabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, munthuyu asenze kuchimwa kwake.


Koma Yesu anangokhala chete. Ndipo mkulu wa ansembe ananena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Khristu, Mwana wa Mulungu.


amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.


Ndipo iye anati kwa amai wake, Ndalama zija mazana khumi ndi limodzi anakuberani zimene munatembererapo, ndi kunenanso m'makutu mwanga, taonani ndalamazo ndili nazo, ndinazitenga ndine. Pamenepo amai wake anati, Yehova adalitse mwana wanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa