Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 7:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo munthu akakhudza chinthu chodetsa, chodetsa cha munthu, kapena chodetsa cha zoweta, kapena chilichonse chonyansa chodetsa, nakadyako nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, munthuyo achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo munthu akakhudza chinthu chodetsa, chodetsa cha munthu, kapena chodetsa cha zoweta, kapena chilichonse chonyansa chodetsa, nakadyako nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Ndipo wina aliyense akakhudza chinthu chonyansa pa zachipembedzo, kaya nchonyansa cha munthu kapena cha nyama, kapenanso chonyansa china chilichonse, tsono nadyako nyama ya nsembe yachiyanjano yopereka kwa Chauta, munthuyo achotsedwe pakati pa Aisraele anzake.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Ndipo ngati munthu wina akhudza chinthu chodetsedwa, kaya chonyansa cha munthu kapena cha nyama, kapenanso chonyansa china chilichonse, ndipo kenaka nʼkudya nyama ya nsembe yachiyanjano imene ndi ya Yehova, munthu ameneyo achotsedwe pakati anthu a mtundu wake.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 7:21
31 Mawu Ofanana  

Ndipo mwamuna wosadulidwa, wosadulidwa khungu lake, munthuyo amsadze mwa anthu a mtundu wake; waphwanya pangano langa.


Masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda chotupitsa; lingakhale tsiku loyamba muzichotsa chotupitsa m'nyumba zanu; pakuti aliyense wakudya mkate wa chotupitsa kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lachisanu ndi chiwiri, munthu ameneyo adzachotsedwa kwa Israele.


Chisapezeke chotupitsa m'nyumba zanu masiku asanu ndi awiri; pakuti aliyense wakudya kanthu ka chotupitsa, munthuyo adzachotsedwa ku gulu la Israele, angakhale ndiye mlendo kapena wobadwa m'dziko.


Chifukwa chake unene nao, Atero Ambuye Yehova, Mumadyera kumodzi ndi mwazi, mumakwezera maso anu kumafano anu, ndi kukhetsa mwazi; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko cholowa chanu?


Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Taonani, moyo wanga sunadetsedwe, pakuti chiyambire ubwana wanga mpaka tsopano sindinadye chinthu chakufa chokha, kapena chogwidwa ndi chilombo; simunalowanso m'kamwa mwanga nyama yonyansa.


Zokwawa zonse zakuuluka zokhala ndi miyendo inai, muziyesa izi zonyansa.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,


Ndipo munthu aliyense wa mbumba ya Israele, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uliwonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.


Pakuti ndiwo moyo wa nyama zonse, mwazi wake ndiwo moyo wake; chifukwa chake ndinanena kwa ana a Israele, Musamadya mwazi wa nyama iliyonse; pakuti moyo wa nyama yonse ndi mwazi wake; aliyense akaudya adzachotsedwa.


Pakuti aliyense akachita chilichonse cha zonyansa izi, inde amene azichita adzachotsedwa pakati pa anthu a mtundu wao.


koma aliyense akudyako adzasenza mphulupulu yake, popeza waipsa chopatulidwa cha Yehova; ndi munthuyu amsadze, kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.


Ndipo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi kumsadza kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake; popeza anapereka a mbeu zake kwa Moleki, kudetsa nako malo anga opatulika, ndi kuipsa dzina langa lopatulika.


Nena nao, Aliyense wa mbeu zanu zonse mwa mibadwo yanu, akayandikiza zinthu zopatulika, zimene ana a Israele azipatulira Yehova, pokhala ali nacho chomdetsa chake, azimsadza munthuyo pankhope panga; Ine ndine Yehova.


Munthu aliyense wa mbeu za Aroni wokhala ndi khate, kapena kukha, asadyeko zinthu zopatulika, kufikira atayera. Ndipo aliyense wokhudza chinthu chodetsedwa ndi wakufa, kapena mwamuna wogona uipa;


Pakuti munthu aliyense wosadzichepetsa tsiku limenelo, amsadze kwa anthu a mtundu wake.


Koma munthu akadya nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, pokhala nacho chomdetsa, munthuyo achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,


Pakuti aliyense akadya mafuta a nyama imene amabwera nayo ikhale nsembe yamoto ya kwa Yehova, munthu amene akadya awa achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.


Aliyense akadya mwazi uliwonse, munthuyo achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.


Ndipo chilichonse munthu wodetsedwa achikhudza chidzakhala chodetsedwa; ndi munthu wakuchikhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


koma zilizonse zopanda zipsepse kapena mamba musamadya; muziyese zonyansa.


Musamadya chonyansa chilichonse.


Koma Saulo sananene kanthu tsiku lomwelo; chifukwa anaganizira, Kanthu kanamgwera iye, ali wodetsedwa; indedi ali wodetsedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa