Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 15:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo munthu aliyense akakhudza kanthu kalikonse kadali pansi pake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo iye wakunyamula zimenezo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo munthu aliyense akakhudza kanthu kalikonse kadali pansi pake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo iye wakunyamula zimenezo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Aliyense amene akhudze chinthu chilichonse chimene munthuyo adakhalapo, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. Aliyense amene achinyamule, achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ndipo aliyense wokhudza chimene anakhalira munthuyo adzakhala wodetsedwanso mpaka madzulo. Aliyense wonyamula chinthucho achape zovala zake ndi kusamba. Komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 15:10
8 Mawu Ofanana  

Ndidzasamba manja anga mosalakwa; kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova;


Ndipo izi zikudetsani: aliyense akhudza mtembo wake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo;


Ndipo munthu aliyense wakukhayo akamkhudza, osasambatu m'manja m'madzi, atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Ndipo munthu aliyense wakukhudza kama wake azitsuka zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Ndipo wakukhayo akalavulira wina woyera; pamenepo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Ndipo mbereko iliyonse akwerapo wakukhayo ili yodetsedwa.


Ndipo chilichonse munthu wodetsedwa achikhudza chidzakhala chodetsedwa; ndi munthu wakuchikhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa